-
Yeremiya 36:22-24Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
22 Pa nthawiyi nʼkuti mfumu ili mʼnyumba imene inkakhala mʼnyengo yozizira ndipo inkawotha moto wamʼmbaula. Umenewu unali mwezi wa 9.* 23 Yehudi akawerenga zigawo zitatu kapena 4 za mpukutuwo, mfumu inkadula mpukutuwo ndi mpeni wa mlembi nʼkuponya chidutswacho pamoto umene unali mʼmbaula uja. Inachita izi mpaka mpukutu wonsewo unathera pamotopo. 24 Iwo sanachite mantha ndipo mfumu ndi atumiki ake onse amene ankamvetsera mawuwa sanangʼambe zovala zawo.
-