4 Lupanga lidzabwera kudzaukira Iguputo, ndipo anthu a ku Itiyopiya adzachita mantha kwambiri anthu akadzaphedwa ku Iguputo.
Chuma cha Iguputo chidzalandidwa ndipo maziko ake adzagwetsedwa.+
5 Itiyopiya,+ Puti,+ Ludi, anthu onse ochokera mʼmitundu yosiyanasiyana,
Kubi limodzi ndi anthu amʼdziko lapangano,
Onsewa adzaphedwa ndi lupanga.”’