-
Yeremiya 43:12, 13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 Nyumba za milungu* ya ku Iguputo ndidzaziwotcha ndi moto.+ Nebukadinezara adzawotcha nyumbazo nʼkutenga milunguyo kupita nayo kudziko lina. Mʼbusa savutika kuvala chovala chake. Mofanana ndi zimenezi, Nebukadinezara sadzavutika kugonjetsa dziko la Iguputo nʼkuchokako mwamtendere.* 13 Iye adzaphwanyaphwanya zipilala za ku Beti-semesi,* mzinda umene uli ku Iguputo. Ndipo nyumba za milungu* ya ku Iguputo adzaziwotcha ndi moto.”’”
-