12 Ine ndidzadutsa mʼdziko la Iguputo usiku umenewo nʼkupha mwana aliyense woyamba kubadwa mʼdziko la Iguputo, mwana wa munthu kapena wa chiweto.+ Ndipo ndidzapereka chiweruzo pa milungu yonse ya mu Iguputo.+ Ine ndine Yehova.
12 Nyumba za milungu* ya ku Iguputo ndidzaziwotcha ndi moto.+ Nebukadinezara adzawotcha nyumbazo nʼkutenga milunguyo kupita nayo kudziko lina. Mʼbusa savutika kuvala chovala chake. Mofanana ndi zimenezi, Nebukadinezara sadzavutika kugonjetsa dziko la Iguputo nʼkuchokako mwamtendere.*
25 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti: ‘Tsopano ndilanga Amoni+ wa ku No,*+ Farao, Iguputo pamodzi ndi milungu yake+ ndi mafumu ake. Inde ndilanga Farao ndi onse amene amamukhulupirira.’+