Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Salimo 136:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  3 Yamikani Mbuye wa ambuye,

      Chifukwa chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.

  • Salimo 136:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  5 Iye anapanga kumwamba mwaluso,*+

      Chifukwa chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.

  • Yesaya 40:22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 Pali winawake amene amakhala pamwamba pa dziko lapansi lomwe ndi lozungulira,+

      Ndipo amene amakhala mʼdzikolo ali ngati ziwala.

      Iye anatambasula kumwamba ngati nsalu yopyapyala,

      Ndipo anakufutukula ngati tenti yoti azikhalamo.+

  • Yeremiya 51:15, 16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Iye ndi Mulungu amene anapanga dziko lapansi pogwiritsa ntchito mphamvu zake,

      Amene anakhazikitsa dziko lapansi pogwiritsa ntchito nzeru zake+

      Amenenso anatambasula kumwamba chifukwa cha kuzindikira kwake.+

      16 Mawu ake akamveka,

      Madzi akumwamba amachita mkokomo,

      Ndipo amachititsa mitambo* kukwera kuchokera kumalekezero a dziko lapansi.

      Iye amachititsa kuti kukamagwa mvula mphezi zizingʼanima

      Ndipo amatulutsa mphepo mʼnyumba zake zosungira.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena