Deuteronomo 30:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Yehova Mulungu wanu adzabweza kwawo anthu a mtundu wanu amene anagwidwa nʼkupita kudziko lina,+ ndipo adzakuchitirani chifundo+ nʼkukusonkhanitsaninso pamodzi kuchokera pakati pa anthu onse kumene Yehova Mulungu wanu anakubalalitsirani.+ Deuteronomo 30:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Yehova Mulungu wanu adzakubweretsani mʼdziko limene makolo anu analitenga kuti likhale lawo, ndipo lidzakhala lanu. Iye adzachititsa kuti zinthu zikuyendereni bwino ndipo adzakuchulukitsani kwambiri kuposa makolo anu.+ Amosi 9:14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 Ndidzasonkhanitsa ndi kubwezeretsa anthu anga Aisiraeli amene anatengedwa kupita ku ukapolo.+Iwo adzamanga mizinda imene ili yabwinja nʼkumakhalamo.+Adzalima minda ya mpesa nʼkumwa vinyo wake.+Adzalimanso minda nʼkudya zipatso zake.’+ Zekariya 10:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 ‘Ndidzawaitana ndi likhweru nʼkuwasonkhanitsa pamodzi.Popeza ndidzawawombola,+ iwo adzachuluka.Ndipo adzapitiriza kuchuluka.
3 Yehova Mulungu wanu adzabweza kwawo anthu a mtundu wanu amene anagwidwa nʼkupita kudziko lina,+ ndipo adzakuchitirani chifundo+ nʼkukusonkhanitsaninso pamodzi kuchokera pakati pa anthu onse kumene Yehova Mulungu wanu anakubalalitsirani.+
5 Yehova Mulungu wanu adzakubweretsani mʼdziko limene makolo anu analitenga kuti likhale lawo, ndipo lidzakhala lanu. Iye adzachititsa kuti zinthu zikuyendereni bwino ndipo adzakuchulukitsani kwambiri kuposa makolo anu.+
14 Ndidzasonkhanitsa ndi kubwezeretsa anthu anga Aisiraeli amene anatengedwa kupita ku ukapolo.+Iwo adzamanga mizinda imene ili yabwinja nʼkumakhalamo.+Adzalima minda ya mpesa nʼkumwa vinyo wake.+Adzalimanso minda nʼkudya zipatso zake.’+
8 ‘Ndidzawaitana ndi likhweru nʼkuwasonkhanitsa pamodzi.Popeza ndidzawawombola,+ iwo adzachuluka.Ndipo adzapitiriza kuchuluka.