Genesis 16:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Pambuyo pake, mngelo wa Yehova anakumana ndi Hagara mʼchipululu ali pakasupe wamadzi. Kasupeyo anali panjira yopita ku Shura.+ Genesis 16:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Ndiyeno Hagara anapemphera kwa Yehova* kuti: “Inu ndinu Mulungu amene amaona chilichonse.”+ Ananenanso kuti: “Kodi nanenso pano ndaona amene amatha kundionayo?” Miyambo 15:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Maso a Yehova ali paliponse,Amaona anthu oipa ndi abwino omwe.+ Amosi 9:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Akadzakumba Manda* kuti abisalemo,Ndidzawatulutsa ndi dzanja langa.Ndipo akadzakwera kumwamba,Ndidzawatsitsira pansi. Aheberi 4:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Palibe cholengedwa chimene Mulungu sangathe kuchiona.+ Chifukwa kwa iye zinthu zonse zili poonekera ndipo amatha kuziona bwinobwino moti ifeyo tidzayankha kwa Mulunguyo pa zochita zathu.+
7 Pambuyo pake, mngelo wa Yehova anakumana ndi Hagara mʼchipululu ali pakasupe wamadzi. Kasupeyo anali panjira yopita ku Shura.+
13 Ndiyeno Hagara anapemphera kwa Yehova* kuti: “Inu ndinu Mulungu amene amaona chilichonse.”+ Ananenanso kuti: “Kodi nanenso pano ndaona amene amatha kundionayo?”
2 Akadzakumba Manda* kuti abisalemo,Ndidzawatulutsa ndi dzanja langa.Ndipo akadzakwera kumwamba,Ndidzawatsitsira pansi.
13 Palibe cholengedwa chimene Mulungu sangathe kuchiona.+ Chifukwa kwa iye zinthu zonse zili poonekera ndipo amatha kuziona bwinobwino moti ifeyo tidzayankha kwa Mulunguyo pa zochita zathu.+