2 “Iwe mwana wa munthu, losera zokhudza aneneri a mu Isiraeli+ ndipo anthu amene akulosera zamʼmutu mwawo+ uwauze kuti, ‘Imvani mawu a Yehova. 3 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Tsoka kwa aneneri opusa, amene akungolosera zamʼmutu mwawo pamene sanaone chilichonse.+