-
Ezekieli 25:12, 13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Edomu wabwezera zoipa kwa nyumba ya Yuda ndipo wapalamula mlandu waukulu chifukwa chowabwezera.+ 13 Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Nditambasulanso dzanja langa nʼkulanga Edomu ndipo ndipha anthu ndi ziweto mʼdzikolo, moti ndidzalisandutsa bwinja.+ Anthu adzaphedwa ndi lupanga kuyambira ku Temani mpaka ku Dedani.+
-
-
Ezekieli 36:5Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
5 Mawu amene Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, akuwauza ndi akuti: ‘Ndidzadzudzula anthu a mitundu ina amene anapulumuka komanso Edomu yense nditakwiya kwambiri.+ Ndidzadzudzula amene anatenga dziko langa kuti likhale lawo akusangalala kwambiri komanso akunyoza+ nʼcholinga choti dzikolo ndi malo ake odyetserako ziweto zikhale zawo.’”’+
-