Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 32:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 32 Mose ali mʼphirimo, anthu anaona kuti akuchedwa kutsika.+ Choncho anthuwo anasonkhana kwa Aroni nʼkumuuza kuti: “Tipangire mulungu woti atitsogolere,+ chifukwa sitikudziwa zimene zachitikira Mose, amene ankatitsogolera pochoka ku Iguputo.”

  • Ekisodo 32:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Kenako iye analandira golideyo kuchokera kwa anthuwo ndipo pogwiritsa ntchito chosemera, anapanga fano* la mwana wa ngʼombe.+ Zitatero iwo anayamba kunena kuti: “Uyu ndi Mulungu wanu, Aisiraeli inu, amene anakutulutsani mʼdziko la Iguputo.”+

  • Numeri 25:1, 2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 Pa nthawi imene Aisiraeli ankakhala ku Sitimu,+ anayamba kuchita chiwerewere ndi akazi a ku Mowabu.+ 2 Akaziwo anaitana Aisiraeliwo kuti azikapereka nsembe kwa milungu yawo+ ndipo Aisiraeliwo anayamba kudya nsembezo komanso kugwadira milungu ya Amowabu.+

  • Machitidwe 7:42
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 42 Choncho Mulungu anawasiya kuti atumikire magulu akumwamba+ ngati mmene malemba amanenera mʼbuku la Aneneri. Malembawo amati, ‘Anthu inu a nyumba ya Isiraeli, kodi mʼchipululu muja munkapereka kwa ine nsembe ndi zopereka zina kwa zaka 40?

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena