-
Ezekieli 29:19, 20Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
19 Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Ine ndikupereka dziko la Iguputo kwa Nebukadinezara* mfumu ya Babulo.+ Iye adzatenga chuma cha dzikolo komanso kulanda zinthu zake zochuluka. Zimenezi zidzakhala malipiro a asilikali ake.
20 Ndimupatsa dziko la Iguputo monga chipukutamisozi pa ntchito imene anagwira pomenyana ndi Turo, chifukwa iwo anachita zimene ine ndinkafuna,’+ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.
-