-
Ezekieli 25:12, 13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Edomu wabwezera zoipa kwa nyumba ya Yuda ndipo wapalamula mlandu waukulu chifukwa chowabwezera.+ 13 Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Nditambasulanso dzanja langa nʼkulanga Edomu ndipo ndipha anthu ndi ziweto mʼdzikolo, moti ndidzalisandutsa bwinja.+ Anthu adzaphedwa ndi lupanga kuyambira ku Temani mpaka ku Dedani.+
-
-
Malaki 1:4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 “Ngakhale kuti Edomu akunena kuti, ‘Ife tawonongedwa, koma tibwerera nʼkukamanga malo athu owonongedwawo,’ Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti, ‘Iwo apita kukamanga, koma ine ndikagwetsa. Anthu adzatchula malo awowo kuti “dera la zoipa” ndipo iwowo adzatchedwa “anthu okanidwa ndi Yehova mpaka kalekale.”+
-