-
Chivumbulutso 5:9, 10Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Iwo ankaimba nyimbo yatsopano+ yakuti: “Inu ndinu woyenera kutenga mpukutuwo ndi kumatula zidindo zake zomatira, chifukwa munaphedwa ndipo ndi magazi anu munagula anthu kuti atumikire Mulungu.+ Anthuwo ndi ochokera mu fuko lililonse, chilankhulo chilichonse, mtundu uliwonse ndi dziko lililonse.+ 10 Ndipo munawapanga kuti akhale mafumu+ ndi ansembe a Mulungu wathu,+ moti adzakhala mafumu+ olamulira dziko lapansi.”
-
-
Chivumbulutso 20:4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 Kenako ndinaona mipando yachifumu ndipo amene anakhala pamipandoyo anapatsidwa mphamvu zoweruza. Ndinaona miyoyo ya anthu amene anaphedwa chifukwa chochitira umboni za Yesu komanso chifukwa cholankhula za Mulungu. Inde, ndinaona miyoyo ya anthu amene sanalambire chilombo kapena chifaniziro chake ndipo sanalandire chizindikiro pazipumi zawo ndi padzanja lawo.+ Iwo anakhalanso ndi moyo ndipo analamulira monga mafumu limodzi ndi Khristu+ kwa zaka 1,000.
-