-
Nehemiya 9:17Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
17 Iwo anakana kumvera+ ndipo sanakumbukire zinthu zodabwitsa zimene munawachitira. Mʼmalomwake anaumitsa khosi ndipo anasankha munthu woti awatsogolere pobwereranso ku ukapolo ku Iguputo.+ Koma inu ndinu Mulungu wokonzeka kukhululuka, wachisomo, wachifundo, wosakwiya msanga ndiponso wachikondi chokhulupirika*+ chochuluka, choncho simunawasiye.+
-
-
Mika 7:18, 19Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
18 Kodi pali Mulungu winanso wofanana ndi inu,
Amene amakhululukira zolakwa ndi machimo+ a anthu ake otsala omwe ndi cholowa chake?+
Inu simudzakhalabe wokwiya mpaka kalekale,
Chifukwa mumakonda chikondi chokhulupirika.+
19 Inu mudzatichitiranso chifundo+ ndipo mudzagonjetsa* zolakwa zathu.
Machimo athu onse mudzawaponya mʼnyanja pamalo ozama.+
-