-
Yeremiya 50:4, 5Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 “Mʼmasiku amenewo ndiponso pa nthawi imeneyo anthu a ku Isiraeli komanso anthu a ku Yuda adzabwera limodzi,”+ akutero Yehova. “Iwo azidzayenda akulira+ ndipo onse pamodzi adzafunafuna Yehova Mulungu wawo.+ 5 Iwo adzafunsira njira yopita ku Ziyoni nkhope zawo zitayangʼana kumeneko.+ Iwo adzanena kuti, ‘Bwerani, tiyeni tikhalenso anthu a Yehova pochita pangano limene lidzakhalapo mpaka kalekale lomwe silidzaiwalika.’+
-