Maliko 13:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Koma pamene akupita nanu kukakuperekani, musafulumire kuda nkhawa kuti mukanena chiyani. Zimene mukapatsidwe mu ola lomwelo, mukanene zomwezo chifukwa wolankhula si inu, koma mzimu woyera.+ Luka 12:11, 12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Akapita nanu kumabwalo amilandu,* kwa akuluakulu aboma komanso kwa olamulira, musade nkhawa kuti mukadziteteza bwanji kapena mukanena chiyani,+ 12 chifukwa mzimu woyera udzakuphunzitsani mu ola lomwelo zimene mukuyenera kunena.”+ Luka 21:14, 15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 Choncho tsimikizirani mʼmitima yanu kuti musachite kukonzekera zoti mukayankhe podziteteza,+ 15 chifukwa ine ndidzakuuzani mawu oti munene komanso ndidzakupatsani nzeru zimene otsutsa anu onse sadzatha kuzikana kapena kuzitsutsa.+
11 Koma pamene akupita nanu kukakuperekani, musafulumire kuda nkhawa kuti mukanena chiyani. Zimene mukapatsidwe mu ola lomwelo, mukanene zomwezo chifukwa wolankhula si inu, koma mzimu woyera.+
11 Akapita nanu kumabwalo amilandu,* kwa akuluakulu aboma komanso kwa olamulira, musade nkhawa kuti mukadziteteza bwanji kapena mukanena chiyani,+ 12 chifukwa mzimu woyera udzakuphunzitsani mu ola lomwelo zimene mukuyenera kunena.”+
14 Choncho tsimikizirani mʼmitima yanu kuti musachite kukonzekera zoti mukayankhe podziteteza,+ 15 chifukwa ine ndidzakuuzani mawu oti munene komanso ndidzakupatsani nzeru zimene otsutsa anu onse sadzatha kuzikana kapena kuzitsutsa.+