10 Kenako anawauza kuti: “Mtundu udzaukirana ndi mtundu wina+ ndipo ufumu udzaukirana ndi ufumu wina.+ 11 Kudzachitika zivomerezi zamphamvu ndipo kudzakhala miliri+ ndi njala mʼmalo osiyanasiyana. Kudzaoneka zinthu zoopsa ndipo kumwamba kudzaoneka zizindikiro zodabwitsa.