-
Mateyu 26:55, 56Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
55 Mu ola lomwelo Yesu anafunsa gulu la anthulo kuti: “Bwanji mwabwera kudzandigwira mutatenga malupanga ndi zibonga ngati mukudzalimbana ndi wachifwamba? Tsiku ndi tsiku ndinkakhala pansi mʼkachisi nʼkumaphunzitsa,+ koma simunandigwire.+ 56 Koma zonsezi zachitika kuti zimene aneneri analemba zikwaniritsidwe.”*+ Kenako ophunzira ake onse anamuthawa nʼkumusiya yekha.+
-
-
Luka 22:52, 53Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
52 Ndiyeno Yesu anafunsa ansembe aakulu, oyangʼanira kachisi ndi akulu amene anabwera kudzamugwira kuti: “Bwanji mwabwera ndi malupanga ndi zibonga ngati mukudzalimbana ndi wachifwamba?+ 53 Tsiku ndi tsiku ndinali nanu mʼkachisi+ koma simunandigwire.+ Koma ino tsopano ndi nthawi yanu komanso nthawi ya ulamuliro wamdima.”+
-