Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Salimo 22:16-18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Adani anga andizungulira ngati agalu.+

      Andizungulira ngati gulu la anthu ochita zoipa,+

      Mofanana ndi mkango, iwo akundiluma manja ndi mapazi.+

      17 Ndingathe kuwerenga mafupa anga onse.+

      Adaniwo akuona zimenezi ndipo akundiyangʼanitsitsa.

      18 Iwo akugawana zovala zanga,

      Ndipo akuchita maere pa zovala zanga.+

  • Yesaya 53:1-12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 53 Kodi ndi ndani amene wakhulupirira zinthu zimene anamva kwa ife?*+

      Ndipo kodi dzanja la Yehova+ laonetsedwa kwa ndani?+

       2 Iye adzaphuka ngati nthambi+ pamaso pawinawake* ndiponso ngati muzu wotuluka mʼnthaka youma.

      Saoneka ngati munthu wapadera kapena waulemerero,+

      Ndipo tikamuona, maonekedwe ake si ochititsa chidwi moti ife nʼkukopeka naye.*

       3 Iye ananyozedwa ndipo anthu ankamupewa,+

      Anali munthu amene kupweteka ankakudziwa bwino* ndipo matenda ankawadziwa.

      Zinali ngati kuti nkhope yake yabisika kwa ife.*

      Ananyozedwa ndipo tinkamuona ngati wopanda pake.+

       4 Zoonadi, iye ananyamula matenda athu,+

      Ndipo anasenza zowawa zathu.+

      Koma ifeyo tinkamuona ngati munthu amene wagwidwa ndi matenda, amene walangidwa* ndi Mulungu ndiponso kuzunzidwa.

       5 Koma iye anabayidwa+ chifukwa cha zolakwa zathu.+

      Anaphwanyidwa chifukwa cha zochimwa zathu.+

      Analandira chilango kuti ife tikhale pamtendere,+

      Ndipo chifukwa cha mabala ake ifeyo tinachiritsidwa.+

       6 Tonsefe tikungoyendayenda uku ndi uku ngati nkhosa zosochera.+

      Aliyense akulowera njira yake

      Ndipo Yehova wachititsa kuti zolakwa za tonsefe zigwere pa ameneyo.+

       7 Iye anachitiridwa zankhanza+ ndipo analola kuti azunzidwe,+

      Koma sanatsegule pakamwa pake.

      Anamutengera kumalo oti akamuphere ngati nkhosa,+

      Mofanana ndi nkhosa yaikazi imene yangokhala chete pamene akufuna kuimeta ubweya,

      Ndipo sanatsegule pakamwa pake.+

       8 Iye anaponderezedwa ndipo anatengedwa popanda kuweruzidwa mwachilungamo.

      Ndi ndani amene anaganizira tsatanetsatane wa mʼbadwo wa makolo ake?*

      Popeza iye anadulidwa mʼdziko la anthu amoyo.+

      Iye anakwapulidwa* chifukwa cha zolakwa za anthu anga.+

       9 Anapatsidwa manda* limodzi ndi anthu oipa,+

      Ndipo pamene anafa anaikidwa mʼmanda limodzi ndi anthu olemera,*+

      Ngakhale kuti iye sanalakwe chilichonse*

      Ndipo mʼkamwa mwake munalibe chinyengo.+

      10 Koma Yehova ndi amene anafuna* kuti mtumiki wake aphwanyidwe ndipo anamulola kuti adwale.

      Ngati mungapereke moyo wake kuti ukhale nsembe yakupalamula,+

      Iye adzaona ana ake,* adzakhala ndi moyo kwa nthawi yaitali,+

      Ndipo kudzera mwa iye, zofuna za* Yehova zidzatheka.+

      11 Chifukwa cha kuvutika kwake, iye adzaona zabwino ndipo adzakhutira.

      Chifukwa cha zimene mtumiki wanga wolungama akudziwa,+

      Adzachititsa kuti anthu ambiri azionedwa olungama,+

      Ndipo adzanyamula zolakwa zawo.+

      12 Pa chifukwa chimenechi, ndidzamupatsa gawo pamodzi ndi ambiri,

      Ndipo iye adzagawana ndi amphamvu katundu amene alanda kunkhondo,

      Chifukwa anapereka moyo wake*+

      Ndipo anaikidwa mʼgulu la anthu ochimwa.+

      Ananyamula tchimo la anthu ambiri+

      Ndipo analowererapo kuti athandize anthu ochimwa.+

  • Danieli 9:26
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 26 Pambuyo pa milungu 62 imeneyi, Mesiya adzaphedwa+ ndipo sadzasiya kalikonse.+

      Mtsogoleri adzabwera ndi gulu lake lankhondo ndipo adzawononga mzindawo ndi malo oyera.+ Malo oyerawo adzafafanizidwa ndi madzi osefukira ndipo padzakhala nkhondo mpaka kumapeto. Mogwirizana ndi zimene Mulungu wasankha, kudzakhala chiwonongeko.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena