-
Machitidwe 16:17, 18Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
17 Mtsikana ameneyu ankangotsatira Paulo ndi ifeyo nʼkumafuula kuti: “Anthu awa ndi akapolo a Mulungu Wamʼmwambamwamba+ ndipo akulengeza njira ya chipulumutso kwa inu.” 18 Iye anachita zimenezi kwa masiku ambiri. Kenako Paulo anatopa nazo ndipo anatembenuka nʼkuuza mzimuwo kuti: “Ndikukulamula mʼdzina la Yesu Khristu kuti utuluke mwa mtsikanayu.” Nthawi yomweyo mzimuwo unatuluka.+
-