Mateyu 17:18 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 18 Ndiyeno Yesu anadzudzula chiwandacho ndipo chinatuluka. Nthawi yomweyo mnyamatayo anachira.+ Maliko 1:25, 26 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 25 Koma Yesu anadzudzula mzimuwo kuti: “Khala chete, ndipo tuluka mwa iye!” 26 Choncho mzimu wonyansawo unamuchititsa kuti aphuphe ndipo unafuula mokweza. Kenako unatuluka mwa munthuyo. Maliko 1:34 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 34 Choncho Yesu anachiritsa anthu ambiri amene ankadwala matenda osiyanasiyana+ ndipo anatulutsa ziwanda zambiri. Koma sanalole kuti ziwandazo zilankhule, chifukwa zinkamudziwa kuti ndi Khristu.* Luka 9:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Kenako Yesu anasonkhanitsa atumwi 12 aja nʼkuwapatsa mphamvu ndi ulamuliro pa ziwanda zonse+ komanso kuti azitha kuchiritsa matenda.+ Luka 10:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Kenako anthu okwana 70 aja anabwerera akusangalala ndipo anauza Yesu kuti: “Ambuye, ngakhale ziwanda zimatigonjera tikagwiritsa ntchito dzina lanu.”+
25 Koma Yesu anadzudzula mzimuwo kuti: “Khala chete, ndipo tuluka mwa iye!” 26 Choncho mzimu wonyansawo unamuchititsa kuti aphuphe ndipo unafuula mokweza. Kenako unatuluka mwa munthuyo.
34 Choncho Yesu anachiritsa anthu ambiri amene ankadwala matenda osiyanasiyana+ ndipo anatulutsa ziwanda zambiri. Koma sanalole kuti ziwandazo zilankhule, chifukwa zinkamudziwa kuti ndi Khristu.*
9 Kenako Yesu anasonkhanitsa atumwi 12 aja nʼkuwapatsa mphamvu ndi ulamuliro pa ziwanda zonse+ komanso kuti azitha kuchiritsa matenda.+
17 Kenako anthu okwana 70 aja anabwerera akusangalala ndipo anauza Yesu kuti: “Ambuye, ngakhale ziwanda zimatigonjera tikagwiritsa ntchito dzina lanu.”+