-
Yakobo 4:13-16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 Tamverani inu amene mumanena kuti: “Lero kapena mawa tipita kumzinda wakutiwakuti ndipo tikatha chaka kumeneko. Tikachita malonda kumeneko nʼkupeza phindu.”+ 14 Mumanena zimenezi chonsecho simukudziwa kuti moyo wanu udzakhala wotani mawa.+ Chifukwa muli ngati nkhungu imene imangooneka kwa kanthawi kochepa kenako nʼkuzimiririka.+ 15 Mʼmalomwake muzinena kuti: “Yehova* akalola,+ tikhala ndi moyo ndipo tichita zakutizakuti.” 16 Koma inu mumakonda kunyada komanso kudzitama. Kudzitama konse koteroko ndi koipa.
-