-
Machitidwe 14:12-15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 Choncho Baranaba anayamba kumutchula kuti Zeu, koma Paulo ankamutchula kuti Heme, chifukwa ndi amene ankatsogolera polankhula. 13 Ndiyeno wansembe wa Zeu, amene kachisi wake anali pafupi ndi polowera mumzindawo, anabweretsa ngʼombe zamphongo ndi nkhata zamaluwa pamageti. Iye ankafuna kupereka nsembe pamodzi ndi gulu la anthulo.
14 Koma atumwiwo, Baranaba ndi Paulo, atamva zimenezi anangʼamba malaya awo akunja nʼkuthamanga kukalowa mʼgulu la anthu lija akufuula kuti: 15 “Anthu inu, mukuchitiranji zimenezi? Ifenso ndife anthu okhala ndi zofooka ngati inu nomwe.+ Tikulengeza uthenga wabwino kwa inu kuti musiye zinthu zachabechabezi nʼkuyamba kulambira Mulungu wamoyo, amene anapanga kumwamba, dziko lapansi, nyanja ndi zonse zokhala mmenemo.+
-
-
Chivumbulutso 19:10Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 Zitatero ndinagwada pansi nʼkuwerama patsogolo pa mapazi ake kuti ndimulambire. Koma iye anandiuza kuti: “Samala! Usachite zimenezo!+ Inetu ndangokhala kapolo mnzako ndi wa abale ako amene ali ndi ntchito yochitira umboni za Yesu.+ Lambira Mulungu,+ chifukwa cholinga cha maulosi ndi kuchitira umboni zokhudza Yesu.”+
-
-
Chivumbulutso 22:8, 9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Ine Yohane, ndi amene ndinamva komanso kuona zinthu zimenezi. Nditamva komanso kuona zinthu zimenezi, ndinagwada nʼkuwerama pamapazi a mngelo amene ankandionetsa zinthu zimenezi kuti ndimulambire. 9 Koma iye anandiuza kuti: “Samala! Usachite zimenezo! Inetu ndangokhala kapolo mnzako, kapolo wa aneneri amene ndi abale ako komanso wa anthu amene akutsatira mawu amumpukutu umenewu. Lambira Mulungu.”+
-