-
1 Petulo 5:2-4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 Wetani gulu la nkhosa za Mulungu+ zomwe zili mʼmanja mwanu. Monga oyangʼanira, muzigwira ntchito yanu, osati mokakamizika koma mofunitsitsa monga atumiki a Mulungu.+ Muziigwira ndi mtima wonse, osati chifukwa chofuna kupindulapo kenakake.+ 3 Musamachite zinthu ngati mafumu pakati pa anthu a Mulungu,*+ koma muzipereka chitsanzo chabwino kwa gulu la nkhosa.+ 4 Ndipo mʼbusa wamkulu+ akadzaonekera, mudzalandira mphoto* yosawonongeka yomwe ndi yaulemerero.+
-