-
Machitidwe 17:6, 7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
6 Atalephera kuwapeza, anakokera Yasoni ndi abale ena kwa olamulira a mzindawo, akufuula kuti: “Anthu awa, amene ayambitsa mavuto kwina konseku, tsopano akupezekanso kuno.+ 7 Ndipo Yasoni wawalandira ngati alendo ake. Anthu onsewa akuchita zotsutsana ndi malamulo a Kaisara. Eti akunena kuti kulinso mfumu ina dzina lake Yesu.”+
-