6 Choncho mkokomowu utamveka, panasonkhana gulu lalikulu la anthu. Iwo anadabwa kwambiri, chifukwa aliyense anawamva akulankhula mʼchilankhulo chake. 7 Zimenezi zinawadabwitsa kwambiri moti anayamba kufunsana kuti: “Anthuni, kodi onse akulankhulawa si anthu a ku Galileya?+