-
Aroma 15:18, 19Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
18 Sindidzalankhula chilichonse chimene ndachita pandekha, koma zokhazo zimene Khristu wachita ndi kulankhula kudzera mwa ine kuti ndithandize anthu a mitundu ina kukhala omvera. 19 Iwo akhala omvera chifukwa cha zodabwitsa zamphamvu ndiponso zizindikiro+ zimene mzimu wa Mulungu wachita. Choncho ndalalikira mokwanira uthenga wabwino wonena za Khristu kuyambira ku Yerusalemu mpaka ku Iluriko.+
-
-
1 Akorinto 4:20Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
20 Chifukwa Ufumu wa Mulungu si nkhani ya mawu, koma mphamvu.
-
-
1 Atesalonika 1:5Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
5 Tikutero chifukwa pamene tinkalalikira uthenga wabwino kwa inu, sitinkangolankhula basi, koma uthengawo unali wamphamvu, unabwera ndi mzimu woyera komanso tinalalikira motsimikiza mtima kwambiri. Inunso mukudziwa zimene tinakuchitirani pofuna kukuthandizani.
-