-
Aroma 16:25, 26Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
25 Mulungu angakulimbitseni pogwiritsa ntchito uthenga wabwino umene ndikulengeza ndiponso uthenga wonena za Yesu Khristu umene ukulalikidwa. Uthengawu ndi wogwirizana ndi zimene zaululidwa zokhudza chinsinsi chopatulika+ chimene chakhala chobisika kwa nthawi yaitali. 26 Koma tsopano chinsinsi chimenechi chaululidwa ndipo anthu a mitundu yonse achidziwa kudzera mʼMalemba aulosi. Zimenezi nʼzogwirizana ndi lamulo la Mulungu wamuyaya. Cholinga chake nʼchakuti anthu a mitundu yonse azimumvera mwa chikhulupiriro.
-
-
Aefeso 3:8, 9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Kukoma mtima kwakukulu kumeneku kunaperekedwa kwa ine, munthu wamngʼono pondiyerekeza ndi wamngʼono kwambiri pa oyera onse.+ Ndinapatsidwa kukoma mtima kumeneku+ kuti ndilengeze kwa anthu a mitundu ina uthenga wabwino wonena za chuma chopanda polekezera cha Khristu, 9 ndiponso kuti ndithandize aliyense kuti aone mmene chinsinsi chopatulikacho+ chikuyendetsedwera. Kwa zaka zambiri, Mulungu amene analenga zinthu zonse, wakhala akubisa chinsinsi chimenechi.
-