-
Aroma 13:8, 9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Anthu inu musamakhale ndi ngongole iliyonse kwa munthu aliyense, kupatulapo kukondana,+ popeza amene amakonda munthu mnzake wakwaniritsa lamulo.+ 9 Chifukwa malamulo onena kuti, “usachite chigololo,+ usaphe munthu,+ usabe,+ usasirire mwansanje,”+ ndiponso lamulo lina lililonse limene lilipo, chidule chake chili mʼmawu awa akuti: “Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.”+
-