Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yohane 17:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Ndipo ine ndikudziyeretsa chifukwa cha iwo, kuti iwonso ayeretsedwe ndi choonadi.

  • Aefeso 5:25-27
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 Amuna inu, pitirizani kukonda akazi anu+ ngati mmenenso Khristu anakondera mpingo nʼkudzipereka yekha chifukwa cha mpingowo,+ 26 nʼcholinga choti auyeretse pousambitsa mʼmadzi a mawu a Mulungu.+ 27 Anachita zimenezi kuti iyeyo alandire mpingowo uli wokongola ndiponso waulemerero, wopanda banga kapena makwinya kapenanso chilichonse cha zinthu zoterezi,+ koma kuti ukhale woyera ndi wopanda chilema.+

  • 2 Atesalonika 2:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Komabe, tiyenera kumathokoza Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu, abale amene Yehova* amakukondani, chifukwa Mulungu anakusankhani kuchokera pachiyambi+ kuti mudzapulumuke. Anachita zimenezi pokuyeretsani+ ndi mzimu wake komanso chifukwa munakhulupirira choonadi.

  • 1 Petulo 1:15, 16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Koma mofanana ndi Woyera amene anakuitanani, inunso khalani oyera mʼmakhalidwe anu onse,+ 16 chifukwa Malemba amati: “Mukhale oyera, chifukwa ine ndine woyera.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena