-
Afilipi 2:29, 30Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
29 Ndiye monga mwa nthawi zonse, mulandireni ndi manja awiri ngati mmene mumachitira polandira otsatira a Ambuye. Mumulandire mwachimwemwe ndipo abale ngati amenewa muziwalemekeza kwambiri,+ 30 chifukwa anatsala pangʼono kufa pamene ankagwira ntchito ya Khristu* ndipo anaika moyo wake pachiswe* kuti adzanditumikire mʼmalo mwa inu, popeza simukanatha kubwera kuno kuti mudzandithandize.+
-