-
Chivumbulutso 13:16-18Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
16 Chilombocho chinakakamiza anthu onse, olemekezeka ndi onyozeka, olemera ndi osauka, mfulu ndi akapolo, kuti aikidwe chizindikiro padzanja lawo lamanja kapena pachipumi pawo.+ 17 Chinachita zimenezi kuti aliyense asathe kugula kapena kugulitsa, kupatulapo ngati ali ndi chizindikirocho, dzina+ la chilombo kapena nambala ya dzina lake.+ 18 Apa mʼpamene pakufunika nzeru: Amene ali ndi nzeru awerengere nambala ya chilombocho, chifukwa ndi nambala ya munthu. Nambala yake ndi 666.+
-
-
Chivumbulutso 20:4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 Kenako ndinaona mipando yachifumu ndipo amene anakhala pamipandoyo anapatsidwa mphamvu zoweruza. Ndinaona miyoyo ya anthu amene anaphedwa chifukwa chochitira umboni za Yesu komanso chifukwa cholankhula za Mulungu. Inde, ndinaona miyoyo ya anthu amene sanalambire chilombo kapena chifaniziro chake ndipo sanalandire chizindikiro pazipumi zawo ndi padzanja lawo.+ Iwo anakhalanso ndi moyo ndipo analamulira monga mafumu limodzi ndi Khristu+ kwa zaka 1,000.
-