Salimo
Salimo la Davide.
Mukakhala chete pamene ndikukuitanani,
Ndidzafanana ndi anthu amene akutsikira kudzenje la manda.+
2 Imvani mawu anga ochonderera pamene ndikufuulira inu kuti mundithandize,
Pamene ndikukweza manja anga, nditayangʼana kumene kuli chipinda chamkati chamʼmalo anu opatulika.+
3 Musandikokolole pamodzi ndi anthu oipa, amene amachita zopweteka anzawo,+
Anthu amene amalankhula mawu amtendere ndi anzawo, koma mʼmitima yawo muli zinthu zoipa.+
Abwezereni mogwirizana ndi ntchito za manja awo,
Mogwirizana ndi zimene achita.+
Mulungu adzawagwetsa ndipo sadzawamanga.
6 Atamandike Yehova,
Chifukwa iye wamva kuchonderera kwanga kopempha thandizo.
Iye wandithandiza, moti mtima wanga ukusangalala.
Choncho ndidzamutamanda ndi nyimbo yanga.
8 Yehova ndi mphamvu kwa anthu ake,
Iye ndi malo achitetezo, amapereka chipulumutso chachikulu kwa wodzozedwa wake.+
9 Pulumutsani anthu anu, ndipo dalitsani cholowa chanu.+
Mukhale mʼbusa wawo ndipo muwanyamule mʼmanja mwanu mpaka kalekale.+