1 Dzina la Mulungu M’Malemba Achiheberi Komanso M’Malemba Achigiriki
“Yehova.” Chiheberi, יהוה (YHWH kapena JHVH)
“Yehova” (Chiheberi, יהוה, YHWH), ndi dzina lenileni la Mulungu ndipo likupezeka koyamba pa Ge 2:4. Dzina la Mulunguli ndi mneni wosonyeza chinthu chimene chimachititsa kuti chinachake chichitike. Mneni wachiheberi ameneyu הוה (ha·wahʹ, “kukhala”) amanenanso za chinthu chimene chikuchitikabe. Choncho dzina la Mulungu limeneli limatanthauza kuti “Iye Amachititsa Kukhala.” Dzina limeneli limasonyeza kuti nthawi zonse Yehova amadzichititsa kukhala Wokwaniritsa malonjezo ake, amenenso nthawi zonse amakwaniritsa zolinga zake.
Chipongwe chachikulu chimene omasulira amakono achitira Mulungu, amene ndi Mlembi wa Malemba Opatulika ndicho kuchotsa kapena kubisa dzina lapaderali la Mulungu. Dzina limeneli kwenikweni limapezeka m’Malemba Achiheberi m’malo okwana 6,828. M’malo amenewa anagwiritsa ntchito mawu akuti יהוה (YHWH kapena JHVH), zomwe ndi zilembo zinayi zoimira dzina la Mulungu. Pogwiritsa ntchito dzina lakuti “Yehova” tatsatira kwambiri zimene zinalembedwa m’mipukutu yoyambirira ndipo sitinatsatire zimene ena anachita zolemba mayina aulemu monga “Ambuye,” “Adonai” kapena “Mulungu” pamene panali zilembo zinayi zoimira dzina la Mulungu.
Dzina lakuti “Yehova” likupezeka m’malo okwana 6,973 m’Malemba Achiheberi mu Baibulo la Dziko Latsopano. Kwenikweni dzina limeneli limapezeka m’malo okwana 6,828 m’Malemba Achiheberi kuphatikizapo malo atatu pamene dzinali analiphatikiza ndi mawu ena. (Ge 22:14; Eks 17:15; Owe 6:24) M’malo ena 6 dzinali likupezeka m’timitu ta m’buku la Masalimo (7; 18 [m’malo atatu]; 36; 102). M’malo onse 6,828 zilembo zinayi zoimira dzina la Mulungu, tazimasulira kuti “Yehova” kupatula pa Owe 19:18 pamene talemba kuti “kwanga” m’malo mwa dzina la Mulungu. Kuwonjezera apo, tabwezeretsa dzina la Mulungu pa De 30:16; 2Sa 15:20; ndi pa 2Mb 3:1 malinga ndi zimene zili m’Baibulo la Septuagint. Tabwezeretsanso dzina la Mulungu pa Yes 34:16 ndi pa Zek 6:8 pamene dzina lakuti “Yehova” linayenera kulembedwa m’malo mwa mawu akuti “panga” ndi “wanga.” Komanso tabwezeretsa dzina la Mulungu m’malo ena 141 pamene Asoferi analisintha n’kulembapo ʼAdho·naiʹ kapena ʼElo·himʹ.
Kuti tisadutse malire a ntchito ya womasulira n’kuyamba kufotokozera malemba, tayesetsa kukhala osamala kwambiri polemba dzina la Mulungu m’Malemba Achigiriki. Nthawi zonse tinali kuyamba tafufuza mosamala Malemba Achiheberi monga maziko. Tinafufuzanso mabaibulo achiheberi osiyanasiyana amene alipo omasulira Malemba Achigiriki kuti tione ngati akugwirizana ndi zimene talemba.
M’Malemba Achiheberi komanso mu Septuagint yachigiriki anagwiritsa ntchito zilembo zinayi zachiheberi zoimira dzina la Mulungu (יהוה). Choncho kaya Yesu ndi ophunzira ake anali kuwerenga Malemba m’Chiheberi kapena m’Chigiriki, dzina la Mulungu anali kulipeza m’Malemba amenewo. Yesu anatchula dzina la Mulungu pamene anaimirira m’sunagoge ku Nazareti ndi kuwerenga m’buku la Yesaya pa chaputala 61, mavesi 1 ndi 2 pamene pali zilembo zinayi zoimira dzina la Mulungu. Izi zinali zogwirizana ndi cholinga chake chodziwikitsa dzina la Yehova kwa anthu. Cholinga chimenechi chimaonekera m’pemphero limene anapereka kwa Atate wake lakuti: “Anthu amene munawatenga m’dziko ndi kundipatsa ine ndawadziwitsa dzina lanu. . . . Ine ndachititsa kuti iwo adziwe dzina lanu ndipo ndidzapitiriza kuwadziwitsa dzinalo.”—Yoh 17:6, 26.
M’Malemba Achigiriki a m’Baibulo lino talemba dzina la Mulungu m’malo 237. Tinapeza mabaibulo achiheberi osiyanasiyana amene amasonyeza kuti dzinali linayeneradi kubwezeretsedwa m’malo onse 237 amenewo.