Masalimo
Kwa wotsogolera nyimbo. Salimo la Davide, mtumiki wa Yehova.
3 Mawu a pakamwa pake ndi opweteka ndi achinyengo.+
Wasiya kugwiritsa ntchito nzeru zomuthandiza kuchita zinthu zabwino.+
4 Ali pabedi lake amakonza chiwembu kuti apweteke anzake.+
Amaima panjira yoipa.+
Sapewa kuchita zinthu zoipa.+
6 Inu Mulungu, chilungamo chanu chili ngati mapiri anu.+
Chiweruzo chanu ndi chozama kwambiri ngati madzi akuya.+
Inu Yehova, mumapulumutsa munthu ndiponso nyama.+
7 Inu Mulungu, kukoma mtima kwanu kosatha ndi kwamtengo wapatali!+
Ndipo ana a anthu amabisala mu mthunzi wa mapiko anu.+
8 Amadya ndi kukhuta chakudya chonona m’nyumba mwanu.+
Ndipo mumawamwetsa mumtsinje wa zosangalatsa zanu zambiri.+
10 Pitirizani kusonyeza kukoma mtima kwanu kosatha kwa anthu okudziwani,+
Ndiponso chilungamo chanu kwa anthu owongoka mtima.+