Masalimo
Nyimbo yoimba polira* imene Davide anaimbira Yehova, yonena za mawu a Kusi M’benjamini.
7 Inu Yehova Mulungu wanga,+ ine ndathawira kwa inu.+
Ndipulumutseni kwa onse ondizunza ndipo mundilanditse,+
2 Kuti pasapezeke wondikhadzulakhadzula ngati mmene mkango umachitira,+
Pasapezeke wondikwatula popanda wondilanditsa.+
3 Inu Yehova Mulungu wanga, ngati ndachita cholakwa chilichonse,+
Ngati manja anga achita zosalungama zilizonse,+
4 Ngati munthu wondichitira zabwino ndamubwezera zoipa,+
Kapena ngati ndafunkha zinthu za aliyense wondichitira zoipa amene sanaphule kanthu,+
5 Mdani wanga afunefune moyo wanga,+
Ndipo aupeze ndi kuupondaponda pafumbi.
Ulemerero wanga aukwirire m’fumbi. [Seʹlah.]
6 Nyamukani, inu Yehova, mu mkwiyo wanu.+
Imirirani ndi kukhaulitsa amene andisonyeza mkwiyo ndi kundichitira zoipa.+
Dzukani ndi kundithandiza,+ pakuti mwalamula kuti chiweruzo chiperekedwe.+
7 Mitundu ya anthu isonkhane ndi kukuzungulirani,
Ndipo inu mubwerere kumwamba ndi kuwakhaulitsa.
8 Yehova adzapereka chigamulo ku mitundu ya anthu.+
Ndiweruzeni inu Yehova, mogwirizana ndi chilungamo changa,+
Komanso mogwirizana ndi mtima wanga wosagawanika.+
10 Chishango changa chili ndi Mulungu,+ Mpulumutsi wa anthu owongoka mtima.+
12 Ngati munthu sadzabwerera kusiya zoipa,+ Mulungu adzanola lupanga lake,+
Adzakunga uta wake ndi kukonzekera kulasa.+