Masalimo
Kwa wotsogolera nyimbo pa Gititi.*+ Nyimbo ya Davide.
8 Inu Yehova Ambuye wathu, dzina lanu ndi lalikulu padziko lonse lapansi,+
Inuyo ulemerero wanu ukusimbidwa kumwambamwamba!+
2 M’kamwa mwa ana aang’ono ndi ana oyamwa mwakhazikitsamo zamphamvu,+
Chifukwa cha amene akukuchitirani zoipa.+
Mwatero kuti mugonjetse mdani wanu komanso amene akufuna kukubwezerani zoipa.+
3 Ndikayang’ana kumwamba, ntchito ya zala zanu,+
Mwezi ndi nyenyezi zimene munapanga,+
4 Ndimaganiza kuti: Munthu+ ndani kuti muzimuganizira,+
Ndipo mwana wa munthu wochokera kufumbi ndani kuti muzimusamalira?+
5 Munamuchepetsa pang’ono poyerekeza ndi ena onga Mulungu,*+
Kenako munamuveka ulemerero+ ndi ulemu monga chisoti chachifumu.+
7 Nkhosa, mbuzi ndi ng’ombe zamphongo, zonse zimenezi,+
Komanso zilombo zakutchire.+
8 Mbalame zam’mlengalenga ndi nsomba za m’nyanja,+
Chilichonse choyenda m’njira za pansi pa nyanja.+
9 Inu Yehova Ambuye wathu, dzina lanu ndi lalikulu padziko lonse lapansi!+