Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 1:29
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 29 Tsopano Mulungu anati: “Taonani, ndakupatsani zomera zonse zobala mbewu zapadziko lonse lapansi, ndi mitengo yonse yobala zipatso za mbewu+ kuti zikhale chakudya chanu.+

  • Genesis 9:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Nyama yamoyo iliyonse ikhale chakudya chanu.+ Komanso ndikukupatsani zamasamba zonse kuti zikhale chakudya chanu.+

  • Mateyu 6:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 “Pa chifukwa chimenechi, ndikukuuzani kuti: Lekani kudera nkhawa+ moyo wanu kuti mudzadya chiyani, kapena mudzamwa chiyani, kapenanso kuti mudzavala chiyani.+ Kodi moyo suposa chakudya, ndipo kodi thupi siliposa chovala?+

  • Mateyu 6:30
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 30 Tsopano ngati Mulungu amaveka chotero zomera zakutchire, zimene zimangokhalapo lero lokha, mawa n’kuzisonkheza pamoto, kodi iye sadzakuvekani kuposa pamenepo, achikhulupiriro chochepa inu?+

  • Luka 12:28
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 28 Tsopano ngati Mulungu amaveka chotero zomera zakutchire, zimene zimangokhalapo lero lokha, mawa n’kuzisonkhezera pamoto, kuli bwanji inu, achikhulupiriro chochepa inu! Ndithudi, iye adzakuvekani kuposa pamenepo.+

  • Yohane 3:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 “Pakuti Mulungu anakonda+ kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha,+ kuti aliyense wokhulupirira+ iye asawonongeke,+ koma akhale ndi moyo wosatha.+

  • Machitidwe 14:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Komabe iye sanangokhala wopanda umboni wakuti anachita zabwino.+ Anakupatsani mvula+ kuchokera kumwamba ndi nyengo zimene zokolola zanu zimakhala zambiri. Anadzaza mitima yanu ndi chakudya komanso chimwemwe.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena