Mateyu 8:26 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 26 Koma iye anawafunsa kuti: “N’chifukwa chiyani mukuchita mantha chonchi, anthu achikhulupiriro chochepa inu?”+ Kenako anadzuka n’kudzudzula mphepo ndi nyanjayo, ndipo panachita bata lalikulu.+ Mateyu 14:31 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 31 Nthawi yomweyo Yesu anatambasula dzanja lake ndi kum’gwira dzanja n’kumuuza kuti: “Wachikhulupiriro chochepa iwe, n’chifukwa chiyani wakayikira?”+ Mateyu 16:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Yesu anadziwa zimenezi ndipo ananena kuti: “Inu achikhulupiriro chochepa, mulibe mikate. Ndiye n’chifukwa chiyani mukukambirana zimenezi?+ Luka 12:28 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 28 Tsopano ngati Mulungu amaveka chotero zomera zakutchire, zimene zimangokhalapo lero lokha, mawa n’kuzisonkhezera pamoto, kuli bwanji inu, achikhulupiriro chochepa inu! Ndithudi, iye adzakuvekani kuposa pamenepo.+
26 Koma iye anawafunsa kuti: “N’chifukwa chiyani mukuchita mantha chonchi, anthu achikhulupiriro chochepa inu?”+ Kenako anadzuka n’kudzudzula mphepo ndi nyanjayo, ndipo panachita bata lalikulu.+
31 Nthawi yomweyo Yesu anatambasula dzanja lake ndi kum’gwira dzanja n’kumuuza kuti: “Wachikhulupiriro chochepa iwe, n’chifukwa chiyani wakayikira?”+
8 Yesu anadziwa zimenezi ndipo ananena kuti: “Inu achikhulupiriro chochepa, mulibe mikate. Ndiye n’chifukwa chiyani mukukambirana zimenezi?+
28 Tsopano ngati Mulungu amaveka chotero zomera zakutchire, zimene zimangokhalapo lero lokha, mawa n’kuzisonkhezera pamoto, kuli bwanji inu, achikhulupiriro chochepa inu! Ndithudi, iye adzakuvekani kuposa pamenepo.+