Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g87 9/8 tsamba 28
  • Kuchokera kwa Aŵerengi Athu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuchokera kwa Aŵerengi Athu
  • Galamukani!—1987
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chiyembekezo Kaamba ka Odwala Maganizo
  • Ufuko
  • Kuperewera Kwa Madzi
  • Kuchiritsa Kwapafupi kwa Zironda za M’mimba?
  • Kodi Tsankho Limayamba Bwanji?
    Galamukani!—2009
  • Kodi Dzikoli Likupita Kuti?
    Nsanja ya Olonda—2005
Galamukani!—1987
g87 9/8 tsamba 28

Kuchokera kwa Aŵerengi Athu

Chiyembekezo Kaamba ka Odwala Maganizo

Ndikulemba kulongosola kuyamikira kwanga kaamba ka nkhani zanu pa “Chiyembekezo kaamba ka Odwala Maganizo.” (July 8, 1987) ndikupatsidwa mankhwala tsopano kaamba ka kudwala maganizo. Ndakhala ndi mavuto kwa zaka zambiri, koma osadziŵa chochita, ndinangokhala wopirira nazo. Ndiyeno September yathayi malingaliro anga anaipiratu. Ndinapita ku chipatala kaamba ka kufufuzidwa ndipo ndinapatsidwa mankhwala. Mkhalidwe wanga wawongokera kwenikweni. Ndiri wosangalala kuti munalongosola nsonga yakuti mankhwala sapangitsa chizolowezi ndipo kuti aja omwe amamwa mankhwala sali ofooka. Ndingoyembekeza kuti manyazi amene amagwirizana ndi kulandira mankhwala adzachotsedwapo.

T. K., Japan

Ufuko

Sindimvetsetsa kusuliza kwanu kosaleka kwa ufuko pamene muyesa kusungilira kuima kosadzilowetsa m’ndale zadziko. Chipembedzo, mbiri, ndi lingaliro la ufuko ziri zikhulupiriro zotsogoza za zokumana nazo za munthu. Anthu ambiri amasungilira kuti Kristu mu nthaŵi yake pa dziko lapansi anali wa ufuko wa Chiyuda wotsutsidwa ndi ulamuliro wa Chiroma.

J. M., Scotland

Ponena za ufuko, wodziwa za mbiri yakale wa Chibritishi Arnold Toynbee anati: “Uli mkhalidwe wa malingaliro ku umene timapereka chikhulupiriro chachikulu cha ndale zadziko ku mbali imodzi ya fuko la munthu . . . mosasamala kanthu ndi zotulukapo zimene ichi chingadzakhale nacho pa alendo ambiri afuko la anthu.” Mkonzi Ivo Duchacek anawona kuti: “Ufuko umagawanitsa anthu mu magulu othandizira kusagwirizana.” Mlembi Wamkulu wakale wa UN U Thant anawona kuti: “Mavuto ambiri amene timakumana nawo lerolino ali kaamba ka, kapena chotulukapo cha, mikhalidwe yabodza . . . Pakati pa iyi chiri chikhulupiriro cha ufuko wochepa—‘dziko langa, lokhoza kapena lolakwa.’” Wolemba wotchuka wa ku Argentina Jorge Luis Borges analongosola kuti ufuko “uli kuchita choipa kwakukulu kwa zoipa zonse. Umagawanitsa anthu, umawononga mbali yabwino ya chibadwa cha anthu, umatsogolera ku mkhalidwe woipa m’kugawana kwa chuma.” Ponena za Yesu Kristu, kuima kwake kunalongosoledwa momvekera bwino pa Yohane 18:33, 36 mu kuyankha kwake funso la Pilato: “Iwe ndiwe mfumu ya Ayuda kodi?” Yesu analongosola kuti: “Ufumu wanga suli wa dziko lino lapansi.”—ED.

Kuperewera Kwa Madzi

Chonde nditumizireni makope 200 a kope lanu lakuti “Kodi Tikutheredwa ndi Madzi?” (November 22, 1986, Chingelezi) Mmene kopeli linaliri la pa nthaŵi yake ponena za madzi, ndipo linali lofunika chotani nanga! Ndikuyamikani kaamba ka kukhala kwanu Ogalamuka! ku mkhalidwe woipitsitsawu.

W. J. K., United States

Kuchiritsa Kwapafupi kwa Zironda za M’mimba?

Ndinagwiritsira ntchito madzi monga mankhwala ochiritsa kuchokera pa tsamba 31 la kope lanu la September 22, 1983, (Chingelezi). Ndinali kugwiritsira ntchito Tagamet kwa miyezi ingapo popanda kuchotsa mavuto a m’mimba kapena kuchepetsa kuwawa mokhutiritsa. Ndinaleka mankhwalawo ndipo ndikumwa madzi odzala ndi maaunsensi 16 panthaŵi zotchulidwa m’kope lanu ndiponso panthaŵi iriyonse pamene ndimva kuwawa. Pamene ndinamwa madzi, kuwawa kunatha m’mphindi khumi. M’thaŵi yochepa chabe sindinafune konse mankhwala ochotsa ululu m’mimba, ndipo pa miyezi ingapo sindinafunikire kutsatiranso kuchiritsa kumeneku. Chinandivuta kukhulupirira kuti kuchiritsa kwapafupi koteroku komwe sikunatenge ndi ndalama iriyonse kunagwira ntchito!

C. G., United States

Nsonga yomwe yalozedwako inali ripoti pa ndemanga yothandizira ndi Dr. F. Batmanghelidj yomwe inawonekera mu kope la June 19, 1983, la “Journal of Clinical Gastroenterology.” “Galamukani!” simayamikira m’mpangidwe umodzi wa kuchiritsa kuposa wina koma imafalitsa nsonga zonga zimenezi kokha monga chidziŵitso kwa aŵerengi athu. Sitikulimbikitsa onse odwala zironda za m’mimba kuleka mankhwala awo olembedwa kaamba ka kuchiritsa kwapafupiku kwa zironda za m’mimba, koma tiri osangalala kuwona kuti ena apindula kuchokera m’chidziŵitsochi.—ED.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena