Kumaliyang’ana Dziko
1986—Chaka cha Mtendere?
Chaka chatha chinalengezedwa ndi Mitundu Yogwirizana monga Chaka cha Mtendere wa Mitundu Yonse. Komabe, mu 1986 panali kuwombana kwa zida za nkhondo kochuluka kuzungulira dziko lonse kuposa panthaŵi ina iriyonse chiyambire Nkhondo ya Dziko II. Mapetowa anafikiridwa ndi gulu la ku yuniversiti mu Hamburg lomwe lalembetsa nkhondo za pambuyo pa 1945 ndi zochititsa zake. Kulingana ndi nyuzipepala ya Chigerman Schwäbische Zeitung, ofufuza anaŵerenga nkhondo 37 mkati mwa 1986—zina zomwe zakhala zikuchitika kwa zaka 20.
Mbiri ya Chimfine
“Mumayambukiridwa” ndi kachirombo ka chimfine kamodzi kokha. Pambuyo pake mumakhala wotetezeredwa kwa iko. Koma pali tizirombo 200 tomwe tingapangitse chimfine. Icho ndicho chifukwa chake, pa msinkhu wa zaka 60, anthu ambiri amakhala ndi chimfine kamodzi pa chaka, ngati pangakhale chirichonse, pamene achichepere amakhala nacho kuchokera ku nthaŵi zisanu ndi chimodzi kufika ku nthaŵi zisanu ndi zitatu pa chaka. Kodi tizirombo ta chimfine timafalikira motani? Mwakamodzikamodzi kupyolera mu mpweya kaamba ka kutsokomola kapena kuyetsemula, atero adokotala. Kugwira kwalingaliridwa tsopano kukhala chochititsa chachikulu chakupatsana. Wodwalayo amagwira mphuno yake ndi kuyambutsa tizirombo ndi dzanja lake ku chinthu chirichonse chimene iye amagwira. “Tingapulumuke kwa maora angapo pamanja, pamalo olimba ndi nsalu zominira,” watero Dr. Sheldon L. Spector, profesala wa chipatala cha mankhwala pa U.C.L.A. “Anthu aumoyo wabwino amatenga tiziromboto ndi manja awo ndi kuziyambukiritsa iwo eni mwa kugwira mphuno zawo ndi maso.” Kusamba m’manja kwa kaŵirikaŵiri ndi kugwiritsira ntchito zotetezera tizirombo kwawonedwa kukhala njira yabwino ya kuchinjirizira kuyambutsa kapena kuyambukiridwa ndi chimfine.
Wokonzekeretsedwa ndi Kuwodzera kwa Pamasana?
Munthu akunenedwa kukhala ndi mtundu wina wa koloko ya mkatikati imene imasunga kayendedwe kamphamvu ya kugona kwake, inachitira ripoti tero El Universal, nyuzipepala ya ku Mexico. Ofufuza, Juergen Zullev ndi Scot Campbell a ku Max Planck Psychiatric Institute mu Munich, Germany, ayerekeza kuti munthu ali wokonzekeretsedwa mwakuthupi ndi kuwodzera kwa pamasana kutatu kwa masiku onse kuwonjezera pa nthaŵi ya usiku ya kugona kwa nthaŵi zonse. Komabe, kulingana ndi phunzirolo, munthu wapondereza kufunika kwake kwa kuwodzera kwa pamasana ndi ntchito ndipo ndi kumwa khofi.
Chaka Chatsopano cha Mariya
Chaka chapadera choperekedwa kwa Namwali Mariya chalengezedwa ndi Papa John Paul II. Icho chinayamba mu June ndipo chiri chaka choyamba cha Mariya chomwe chidzasangalalidwa ndi Akatolika chiyambire 1953-54. Chaka chimenecho chinalengezedwa kusangalala ndi chaka cha 100 cha kusunga Chiphunzitso cha Kukhala ndi Pakati Kwangwiro, chimene chimalengeza kuti Mariya anabadwa wopanda uchimo wa choloŵa. Chaka chatsopano cha Mariya, papa ananena kuti, chidzasangalalidwa m’chikonzekero cha “zaka chikwi za chitatu za mbadwo Wachikristu.” Iye anatsiriza kulengeza kwake mwakumati: “May 1987 ikhale chaka chimene anthu potsirizira pake ayika pambali mipatuko ya kumbuyo, chaka m’chimene, mu kukula ndi chikhulupiriro, mtima uliwonse umafuna mtendere.”
Kugalamukanso kwa Chipembedzo
Kodi chipembedzo chikukhalanso ndi mphamvu mu United States. Inde, yatero U.S.News & World Report. “Chiphunzitso chakuti Mulungu ali wakufa chiri chakufa icho chenicho,” inadziŵitsa tero magaziniyo. “Sayansi sinapereke mayankho onse a umoyo.” Anthu omamatira ku chipembedzo akunenedwa tsopano kukhala akudzimva mwa chidaliro ponena za kulongosola kwa chikhulupiriro chawo. Makolo, mwakufunafuna zifuno zokhazikika akudzimva kuti zoperekedwa ndi tchalitchi, zikupatsa ana awo chiphunzitso cha chipembedzo. Ngakhale anthu otchuka mwa ndale zadziko alongosola poyera chipembedzo kukhala magwero apadera m’miyoyo yawo. Masankho amasonyeza kuti chipembedzo chikupeza kufunika mu chitaganya. “Kugwira ntchito kwa chipembedzo kuli kolemekezeka kachiŵirinso,” walongosola tero mphunzitsi wa za chipembedzo Martin Marty. Koma iye wawonjezera kuti: “Palinso zifukwa zabwino za kuwopera chipembedzo: Anthu amapha m’dzina la Mulungu, kapena kupyolera mu zolembedwa za lamulo amadidikiza osakhulupirira ochepa kapena ‘akhulupiriri ena.’”
Mitengo Yopotozedwa
Pamene kuli kwakuti anthu mamiliyoni 800 mu dziko lotukuka kumene “amakhala mu kusauka ndi kulandidwa,” yatero The Courier, “zoposa $1.5 biliyoni pamphindi” zikugwiritsiridwa ntchito kuzungulira dziko lonse pa zotayidwa za nkhondo. Bukhu la UNESCO lapitiriza kunena kuti: “Kwa msilikari aliyense avereji ya zowonongedwa za nkhondo za dziko lonse ziri $20,000. Pa mwana wa msinkhu wa pasukulu aliyense zowonongedwa zaunyinji za maphunziro ziri $380. Kwa anthu 100,000 aliwonse mu dziko pali asilikari 556, koma kokha adokotala 85. Kokha chimodzi mwa makumi asanu cha zowonongedwa za zida pa chaka zingachotsepo njala ya dziko lonse kudzafika mu chaka cha 2000.”
Oyendetsa Ndege Owodzera
Mosasamala kanthu za malamulo otetezera, “oyendetsa ndege za malonda . . . nthaŵi zina . . . amagona pamene akuyendetsa ndege pamaulendo atali a usiku,” inachitira ripoti tero The Mexico City News. “Nthaŵi zina, aliyense mu chipinda choyendetseramo ndege amawodzera panthaŵi imodzi pamene ndege ikuwulukira pa chipangizo cha kudziyendetsa yokha,” walongosola tero wofufuza m’modzi. Dr. Martin C. Moore-Ede, katswiri pa kundandalitsa ntchito ndi kugona, wayika liwongo pa “kusungulumwa ndi ndandanda zosakhala za nthaŵi zonse zomwe zimapanikiza oyendetsa ndege kugwira ntchito pa maora owonjezereka popanda nthaŵi ya kusintha kwathupi lawo.” Moore-Ede wazika kutsiriza kwake pa phunziro lochitidwa pa kampani ya ndege imodzi limodzinso ndi kufunsa okhala mu chipinda choyendetseramo ndege. Mu kuwuluka kodutsa maiko kumodzi kupita ku Los Angeles, ndege inawuluka mamailosi 100 (160 km) modutsa Pacific Ocean pamene othandizira kuyendetsa ndege okhala pansi asanadzutse oyendetsa owodzerawo mwa kuliza mabelu okhala mu chipinda choyenderetsamo ndege. “Pamene muli mu chipinda ndipo mutu wanu ukugunthira uku ndi uko ndipo simungakhoze kukhala ogalamuka,” watero Dr. Moore-Ede, “tangokumbukirani kuti yemwe ali kutsogoloku ali munthu, nayenso.”
Chakudya “Chowala”
Njoka yaitali mapazi atatu (1 m) inabweretsedwa ku chipatala cha matenda a zinyama cha Yuniversite ya ku Florida kaamba ka kufufuza. X ray ya njokayo inavumbula kuti inameza magulobo owala okhala ndi 15 watts. Kali kadyedwe kosakhala kanthaŵi zonse ka njoka, kodi mwatero? Osati ngati anali mazira a nkhuku, akulongosola tero akatswiri a matenda a zinyama, amene akukhulupirira kuti ichi ndi chimene njokayo ingakhale inaganizira magulobowo kukhala. Mosasamala kanthu za chifukwa cha kusinthira kadyedwe kake, magulobowo achotsedwa mwa kuitumbula, yachitira ripoti tero New Scientist. Elliot Jacobson, katswiri wa matenda a zinyama yemwe anagwira ntchito ya kutumbulako, akuyembekeza kuti njokayo ikakhala bwino mokwanira kotero kuti ikabwezeredwe kuthengo.
Matelefoni Okhoza Kutaidwa
Matelefoni angapeputse kukhala kwanu mu chipatala kapena kukuipitsa. Chifukwa chiri chakuti matelefoni angasunge mitundu yambiri ya tizirombo ndipo ali ovuta kuikamo zotetezera. Mu United States odwala ena mamiliyoni aŵiri pa chaka amakhala oyambukiridwa pamene ali mu chipatala—ambiri kupyolera mu kugwiritsira ntchito matelefoni. Phunziro lochitidwa ndi CDC (Centers for Disease Control) mu Atlanta lasonyeza kuti kuchokera pa 20,000 kufika ku 30,000 a iwo adzafa. Tsopano, monga njira yotetezera, zipatala zina zimapatsa odwala awo mafoni a pulasitiki audongo, olongedweratu, amene angakhoze kuwataya kapena kuwatenga kunyumba pambuyo pokhala mu chipatala. Matelefoni okhoza kutaidwa ali ndi mtengo kuchoka pa $5 kufika ku $15 imodzi ndipo angagwire ntchito chaka chimodzi. Kuwagwiritsira ntchito kwathandizanso chipatala kuchepetsako pa zobedwa kapena mafoni owonongedwa.
Mboni Zipatulidwa
Aliyense amene angatsimikizire kukhala “chiwalo champhamvu ndi chokhulupiridwa cha mayanjano a chipembedzo a Mboni za Yehova” ad-zapatulidwa ku ntchito yankhondo. Ichi chinali chosankha choperekedwa ndi Federal Administration Tribunal ya ku Berlin, yatero nyuzipepala ya Chigerman Tagesspiegel. Kulingana ndi malingaliro a oŵeruza, kudzilongosolera kwa chiphunzitso cha chipembedzo cha Mboni kudzalandiridwa tsopano monga umboni wa lamulo wa kukana kwa chikumbumtima kwa ntchito yankhondo.
Zipinda za mu Hotela za Osasuta Fodya
Marestaurant ndi makampani a ndege sali okha mu kupatsa makasitomala nyumba za osasuta fodya. “Mochedwa, mahotela nawonso akukulitsa kukonda kusasuta fodya komwe kwafalikira mu U.S.,” yatero The Wall Street Journal. Kungoyamba ndi zipinda zazing’ono zaudongo ndipo zoikidwa pambali kaamba ka makasitomala omwe amada ndudu ya utsi ndi kununkha kwa ndudu, ambirimbiri tsopano akusunga kufika ku maperesenti 15 a zipinda zawo kukhala zipinda za osasuta fodya ndipo akuyamba kuchirikiza ntchitoyo. Osati kokha kuti yatsimikizira kukhala yofala kwambiri ndi makasitomala komanso imapindulitsa mahotela, popeza chimatenga nthaŵi yochepera pa maperesenti 26 ya kusamalira zipinda zosakhalamo osuta fodya.