Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g88 1/8 tsamba 8-9
  • Ndi Mtsogolo Motani Kaamba ka Ife ndi Ana Athu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ndi Mtsogolo Motani Kaamba ka Ife ndi Ana Athu?
  • Galamukani!—1988
  • Nkhani Yofanana
  • Kupulumutsa Dziko Lapansi ku Kuwonongedwa
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Chikhulupiriro ndi Mtsogolo Mwanu
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Masiku a Kulambira Satana Aŵerengedwa
    Galamukani!—1994
  • Dziko Lopanda Nkhondo Posachedwa
    Galamukani!—1996
Onani Zambiri
Galamukani!—1988
g88 1/8 tsamba 8-9

Ndi Mtsogolo Motani Kaamba ka Ife ndi Ana Athu?

BANJA silingawononge zoposa zimene limapanga ndi kukhalabe lopanda ngongole. Dziko silingalipire zinthu zambiri kuposa pa zimene limabweretsa ndi kukhalabe bwino; ndiponso sitingapitirize kuwononga kwathu malo otizinga kopereŵera. Sitingawononge nthaka yochulukira kuposa imene imapangidwa, kupanga mpweya womwe titulutsa wambiri kuposa umene zomera zingagwiritsire ntchito, kudula mitengo yambiri kuposa imene timabwezeretsa, kuipitsa mpweya wambiri ndi madzi kuposa mmene dziko lapansi lingabwezere. Kupereŵera kwa malo otizinga, monga kupereŵera kwa chuma chadziko, kudzafunikira kuŵerengeredwa. Zidzalipiridwa, kaya monga ndalama ndi kugwirizana kwa mitundu yonse kapena monga miyoyo—yathu ndi ana athu.

Zopangapanga zamakono zapangitsa kuthekera kwa dziko kukhala bwinja. Zikanagwiritsiridwa ntchito kulichinjiriza. Nchifukwa ninji izo sizikutero? Chikondi cha ndalama. Chingakhale pamtengo wamabiliyoni. Dziko lino silingawone—kapena m’dyera lake silidzawona—kuposa pa kusawona kutali kwake kwa zikhumbo za zinthu zakuthupi. Popeza limakana kulipira ndalama, lidzalipira m’kutaya nthaka yapamwamba, kutaya nkhalango, kutaya malo a madzi pansi pa nthaka, mpweya wa nyumba zotentha, madzi a ululu, matenda ochulukirako, miyoyo ya anthu. Ndipo kuti lisungirire ndalama zake, dziko lino likugulitsa mtsogolo mwa ana ake.

Kodi lidzagalamuka mu nthaŵi yake? Yankho la mbiri yakale siliri lotsimikizira, koma yankho la Mulungu liri. Yehova Mulungu iye mwini ananena kuti adzaloŵereramo ndi “kuwononga iwo akuwononga dziko.” (Chivumbulutso 11:18) Adzawachotsa pa dziko iwo okhalitsa bwinja malo otizinga ndi kuwononga kukongola kwake, popeza analilenga ilo kuti likhale lokhutiritsa moyo ndi lokongola. “Kumwamba ndi mpando wanga wachifumu, ndi dziko lapansi ndi choikapo mapazi anga,” iye akutero, ndipo: “Ndidzachititsa malo amapazi anga ulemerero.”—Yesaya 66:1; 60:13.

Analilenga ilo kuti likhalidwe ndi anthu amene amakonda chilungamo—ndipo lidzatero, ndi mamiliyoni omwe anakhalako kale, ndi mamiliyoni omwe ali ndi moyo tsopano, ndi mamiliyoni a ana omwe adzabadwa. Ichi anachilemba m’Mawu ake, Baibulo, ndipo mungadziŵerengere nokha pa Yesaya 45:18 ndi Yohane 5:28, 29.

Kenaka, losamaliridwa ndi aja olikonda, dziko lapansi lidzadzikonzanso ilo lokha kukhala lokongola monga m’mene Mlengi wathu analipatsa ilo pachiyambi. Kenaka anthu olungama ndi ana awo adzakhala ndi mtsogolo, mwaulemerero: “Katsala kanthaŵi, ndipo oipa adzatha pysiti; inde, udzayang’anira mbuto yake nudzapeza palibe koma ofatsa adzalandira dziko lapansi, nadzakondwera nawo mtendere wochuluka. Olungama adzalandira dziko lapansi nadzakhala momwemo kosatha.”—Masalmo 37:10, 11, 29.

Ndipo sadzafa? Ndipo sadzafadi! “Mulungu yekha adzakhala nawo, Mulungu wawo. Ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo, ndipo sipadzakhalanso imfa, ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa, zoyambazo zapita.” (Chivumbulutso 21:3, 4) Zonkitsa kuti nkukhala zowona? Ayi, dziko loipa liripoli liri loipitsitsa kuti likhalebe.—Danieli 2:44.

Koma inu ndi ana anu mungatsale. Yehova Mulungu akuchipangitsa icho kuthekera kupyolera mu dipo la Mwana wake. Kuphunzira za Yehova ndi Mwana wake kudzatanthauza moyo wosatha kaamba ka inu ndi ana anu—moyo m’dziko latsopano momwe mudzakhala chilungamo. (Yohane 3:16; 17:3; 2 Petro 3:13) Umu mungakhale mtsogolo mwachimwemwe kaamba ka inu ndi ana anu. Kaya imo muli tero kapena ayi ziri kwa inu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena