Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w98 4/15 tsamba 9-14
  • Chikhulupiriro ndi Mtsogolo Mwanu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chikhulupiriro ndi Mtsogolo Mwanu
  • Nsanja ya Olonda—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Zinthu Zinali Motani Kumbuyoko?
  • Anthu Alephera Kuthetsa Mavuto
  • Lingaliro la Mboni za Yehova Ponena za Mtsogolo
  • Mtsogolo mwa Ulamuliro wa Anthu
  • Khulupirirani Malonjezo a Yehova
  • Dalirani Yehova Kuti Adzakwaniritsa Chifuno Chake
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Chifuno cha Mulungu Chidzakwaniritsidwa Posachedwapa
    Kodi Moyo Uli ndi Chifuno?
  • Ufumu wa Mulungu—Ulamuliro Watsopano wa Dziko Lapansi
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Yehova Amakwaniritsa Malonjezo Ake kwa Okhulupirika
    Nsanja ya Olonda—1998
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1998
w98 4/15 tsamba 9-14

Chikhulupiriro ndi Mtsogolo Mwanu

“Chikhulupiriro ndicho chikhazikitso cha zinthu zoyembekezeka, chiyesero cha zinthu zosapenyeka.”​—AHEBRI 11:1.

1. Kodi anthu ambiri amafuna tsogolo lotani?

KODI mukufuna kudziŵa zamtsogolo? Anthu ambiri amatero. Amayembekezera kukhala ndi tsogolo lamtendere, lopanda mantha, la makhalidwe abwino, amafuna ntchito yopindulitsa ndi yosangalatsa, ndiponso thanzi labwino ndi moyo wokhalitsa. Mosakayika konse mbadwo uliwonse m’mbiri wakhala ukufuna zinthu zimenezo. Ndipo lerolino, m’dziko lino lodzaza ndi mavuto, mikhalidwe yotero ikufunikadi kwambiri kusiyana ndi kale lonse.

2. Kodi nduna ina inapereka lingaliro lotani ponena za mtsogolo?

2 Pamene mtundu wa anthu ukuyandikira zaka za zana la 21, kodi ilipo njira iliyonse imene mungadziŵire zamtsogolo? Zaka zoposa 200 zapitazo, Patrick Henry, nduna ya boma la America, anatchula njira imodzi yochitira zimenezo. Iye anati: “Ndimadziŵa njira imodzi yokha yodziŵira zamtsogolo, ndiyo kuona zakumbuyo.” Malinga ndi lingaliro limeneli, tsogolo la anthu lingadziŵike bwino mwa zimene anthu anachita kumbuyoko. Ambiri amagwirizana ndi lingaliro limenelo.

Kodi Zinthu Zinali Motani Kumbuyoko?

3. Kodi mbiri yolembedwa imanenanji ponena za ziyembekezo zamtsogolo?

3 Ngati mtsogolo mudzafanana ndi zakumbuyo, kodi mukuona kuti zimenezo nzolimbikitsa? Kodi zinthu zinali kumka nizikhala bwino mtsogolo kwa mibadwo yapitayo? Osati kwenikweni. Mosasamala kanthu za ziyembekezo zimene anthu akhala nazo zaka zikwi zambiri, ndipo mosasamala kanthu za chitukuko m’maiko ena, mbiri yadzala ndi kuponderezana, upandu, chiwawa, nkhondo, ndi umphaŵi. Dziko lapansili layang’anizana ndi mavuto osiyanasiyana, amene makamaka amadza chifukwa cha ulamuliro wosakhutiritsa wa anthu. Baibulo limanena molondola kuti: “Wina apweteka mnzake pomlamulira.”​—Mlaliki 8:9.

4, 5. (a) Kodi nchifukwa ninji anthu anali kuyembekezera zabwino kumayambiriro a zaka za zana la 20? (b) Kodi ziyembekezo zawo zamtsogolo zinayang’anizana ndi chiyani?

4 Zenizeni nzakuti zinthu zoipa m’mbiri ya munthu zimangobwerezabwereza​—koma zimachitika pamlingo waukulu kusiyana ndi zimene zinachitika kale. Zaka zino za zana la 20 zili umboni wa zimenezo. Kodi anthu atengapo phunziro pa zolakwa zakale, ndi kuyesa kusazichitanso? Chabwino, kumayambiriro kwa zaka za zana lino, anthu ambiri anali ndi chikhulupiriro chakuti dziko lidzakhala labwino mtsogolo chifukwa chakuti panthaŵiyo kunali mtendere ndiponso chifukwa cha kupita patsogolo pa zamafakitale, zasayansi, ndi zamaphunziro. Profesa wina wa payunivesite ananena kuti kuchiyambi kwa ma 1900, anthu anakhulupirira kuti nkhondo siidzachitikanso chifukwa “anthu anali otsogola kwambiri.” Ponena za malingaliro amene anthu anali nawo panthaŵiyo, yemwe kale anali nduna yaikulu ya boma la Britain anati: “Zonse zinali kuyenda bwino nthaŵi zonse. Ndi mmene zinthu zinalili m’nthaŵi imene ndinabadwiramo.” Koma kenaka anati: “Mwadzidzidzi, ndiponso mosayembekezereka, mmaŵa wina mu 1914 zonse zinasintha.”

5 Ngakhale kuti ambiri panthaŵiyo anakhulupirira kuti zinthu zidzakhala bwino mtsogolo, atangoloŵa kumene m’zaka za zana latsopanolo, dziko linagwera m’tsoka loipitsitsa lochititsidwa ndi munthu​—Nkhondo Yadziko I. Kungochitira chitsanzo mmene nkhondoyo inalili, talingalirani zimene zinachitika mu 1916 pa kumenyana kwina pamene asilikali a Britain anathira nkhondo asilikali achijeremani pafupi ndi Mtsinje wa Somme ku France. M’maola oŵerengeka chabe asilikali a ku Britain okwanira 20,000 anaphedwa, ndipo asilikali ambirinso achijeremani anaphedwa. Kuphana kwa zaka zinayi kunatayitsa miyoyo ya asilikali pafupifupi mamiliyoni khumi ndi anthu wamba ambiri. Chiŵerengero cha anthu a ku France chinatsika panthaŵi ina chifukwa chakuti panali anthu ambiri amene anaphedwa. Chuma chinawonongeka, zimene zinachititsa Kugwa kwa Chuma Kwakukulu kwa m’ma 1930. Ndicho chifukwa chake ena anati tsiku limene Nkhondo Yadziko I inayamba ndilo tsiku limene dziko linachita msala!

6. Kodi zinthu zinayamba kuyenda bwino itatha Nkhondo Yadziko I?

6 Kodi ndizo zamtsogolo zimene mbadwo umenewo unaziyembekezera? Ayi, sizinali zimenezo mpang’ono pomwe. Ziyembekezo zawo zinaswekeratu; ndipo zimenezo sizinadzetse chabwino chilichonse. Patangopita zaka 21 zokha kuchokera pamene Nkhondo Yadziko I inachitika, kapena kuti mu 1939, tsoka lina lochititsidwanso ndi munthu ndipo loposa loyamba lija linachitika​—Nkhondo Yadziko II. Inatayitsa miyoyo ya anthu pafupifupi 50 miliyoni, amuna, akazi, ndi ana. Mabomba ambirimbiri ophulitsidwa anafafaniza mizinda. M’Nkhondo Yadziko I, asilikali zikwi zambiri anali kuphedwa pakumenyana kumodzi m’maola oŵerengeka chabe, koma m’Nkhondo Yadziko II, mabomba aŵiri okha a atomu anapha anthu oposa 100,000 pamasekondi chabe. Chinthu chimene ambiri amachilingalira kukhala chonyansa kwambiri kuposa zimenezi ndicho kunyonga anthu mamiliyoni ambiri kumene kunachitika m’misasa yachibalo ya Nazi.

7. Kodi zenizeni nziti ponena za zaka za zana lonse lino?

7 Malipoti angapo amanena kuti, ngati tiphatikiza pamodzi nkhondo za pakati pa maiko, nkhondo zachiweniweni, ndi anthu ophedwa ndi maboma awo, onse amene aphedwa m’zaka za zana lino angafike pafupifupi 200 miliyoni. Lipoti lina linanenanso kuti chiŵerengerocho chingafike 360 miliyoni. Tangolingalirani kuopsa kwa zimenezo​—kupweteka kwake, misozi yake, nsautso yake, ndi miyoyo yotayikayo! Kuphatikiza pamenepo, pa avareji, anthu pafupifupi 40,000, amene ambiri ndi ana, amafa tsiku lililonse ndi mavuto ochitika chifukwa cha umphaŵi. Anthu ochuluka kuŵirikiza chiŵerengero chimenecho katatu amafa tsiku lililonse chifukwa cha kutaya mimba. Ndiponso, pafupifupi anthu 1,000 miliyoni ngosauka kwambiri kwakuti satha kupeza chakudya chofunika kuti azigwira ntchito mwamphamvu tsiku ndi tsiku. Zonsezi zili umboni wa zimene ulosi wa Baibulo unaneneratu kuti tikukhala mu “masiku otsiriza” a dongosolo lino loipa la zinthu.​—2 Timoteo 3:1-5, 13; Mateyu 24:3-12; Luka 21:10, 11; Chivumbulutso 6:3-8.

Anthu Alephera Kuthetsa Mavuto

8. Kodi nchifukwa ninji olamulira aumunthu sangathe kuthetsa mavuto a m’dzikoli?

8 Pamene zaka za zana lino la 20 zikufika kumapeto ake, tingaphatikize zochitika zake pamodzi ndi zochitika za m’zaka mazana ambiri apitawo. Ndipo kodi mbiri yonseyo ikutiuzanji? Ikutiuza kuti atsogoleri aumunthu sanayambe athetsapo mavuto aakulu a dzikoli, kuti sakuwathetsa tsopano, ndi kuti sadzawathetsa mtsogolo. Iwo sangathe mpang’ono pomwe kudzetsa mtundu wa tsogolo limene tikufuna, ngakhale atafunitsitsa chotani. Ndipo olamulira ena sali oona mtima; amangofuna udindo ndi ulamuliro kuti akhutiritse dyera lawo lofuna chuma osati kuthandiza ena.

9. Nchifukwa ninji pali chifukwa chabwino chokayikirira kuti asayansi angathetse mavuto a anthu?

9 Kodi sayansi ndiyo ingathetse mavutowo? Zochitika zakale zikusonyeza kuti singathe konse. Asayansi a boma atayira ndalama zambirimbiri, nthaŵi, ndi mphamvu zawo pakupanga zida zoipitsitsa zothira paizoni, zida zoyambitsa matenda ndi mitundu ina ya zida. Maiko, kuphatikizapo amene alibe ndalama zambiri, onse pamodzi amawononga madola oposa 700,000 miliyoni pachaka kugulira zida zankhondo! Ndiponso, ‘kupita patsogolo kwa sayansi’ kwadzetsanso mankhwala ena amene aipitsa mpweya, nthaka, madzi, ndi chakudya.

10. Kodi nchifukwa ninji maphunziro sangadzetse nkomwe tsogolo labwino?

10 Kodi tingakhale ndi chiyembekezo chakuti sukulu za dzikoli zidzathandiza kudzetsa tsogolo labwino mwa kuphunzitsa makhalidwe abwino, kuganizira ena, ndi kukonda mnansi? Ayi. M’malo mwake, amagogomezera za kuphunzitsa ntchito, ndi kupeza ndalama. Amalimbikitsa mzimu wampikisano kwambiri, osati wothandizana; ndipo masukuluwo saphunzitsa mwambo wachikhalidwe. M’malo mwake, ambiri amalola kugonana ndi aliyense amene munthu afuna, zimene zachititsa kuchuluka kwa mimba za atsikana ndi matenda opatsirana mwakugonana.

11. Kodi nchifukwa ninji zili zokayikitsa kuti a zamalonda angadzetse tsogolo labwino?

11 Kodi amalonda aakulu a dzikoli tsiku lina adzasintha maganizo ndi kufuna kusamalira dziko lathuli ndi kusonyeza chikondi kwa ena mwa kupanga zinthu zothandizadi osati zongopezerapo phindu chabe? Sizikuoneka choncho ayi. Kodi adzaleka kupanga maprogramu apawailesi yakanema odzala ndi chiwawa ndi chisembwere zimene zikupitiriza kupotoza maganizo a anthu, makamaka ana? Zochitika zakale sizolimbikitsa mpang’ono pomwe, chifukwa chakuti kwakukulukulu, TV yakhala chimbudzi cha chisembwere, zonyansa, ndi chiwawa.

12. Kodi munthu ali mumkhalidwe wotani ponena za matenda ndi imfa?

12 Ndiponso, ngakhale madokotala atakhala oona mtima chotani, iwo sangathetse matenda ndi imfa. Mwachitsanzo, kumapeto kwa Nkhondo Yadziko I, madokotala analephera kulimbana ndi fuluwenza yachispanya; imene inapha anthu 20 miliyoni kuzungulira dziko lonse. Lerolino, nthenda ya mtima, kansa, ndi matenda ena akupha afalikira kwambiri. Ndipo zipatala zalepheranso kugonjetsa mliri wamakono wa AIDS. Mosiyana ndi zimenezo, lipoti la U.N. lofalitsidwa m’November 1997 linafotokoza kuti chiŵerengero cha anthu amene akutenga kachirombo ka AIDS chaŵirikiza kaŵiri kuposa chiŵerengero cha kumbuyoku. Anthu mamiliyoni ambiri afa kale ndi kachiromboka. M’chaka chaposachedwapa kumbuyoku, anthu ena mamiliyoni atatu anatenga kachiromboka.

Lingaliro la Mboni za Yehova Ponena za Mtsogolo

13, 14. (a) Kodi Mboni za Yehova zimalingalira motani ponena za mtsogolo? (b) Nchifukwa ninji anthu sangadzetse tsogolo labwino?

13 Komabe, Mboni za Yehova zimakhulupirira kuti mtundu wa anthu uli ndi tsogolo labwino, labwino koposa! Koma sizimakhulupirira kuti tsogolo labwino chotero lingabwere mwa zoyesayesa za munthu. M’malo mwake, zimayembekezera kuti Mlengiyo, Yehova Mulungu ndiye adzadzetsa tsogololo. Iye amadziŵa bwino lomwe mmene mtsogolo mudzakhalira, ndipo mudzakhaladi mosangalatsa! Amadziŵanso kuti anthu sangathe kudzetsa tsogolo lotero. Popeza kuti iwo analengedwa ndi Mulungu, iye amadziŵa bwino lomwe zolephera zawo kuposa wina aliyense. M’Mawu ake, amatiuza mosabisa kuti monga momwe anamlengera, munthu sangathe kulamulira bwinobwino popanda chitsogozo chaumulungu. Chilolezo cha Mulungu chakuti anthu adzilamulire popanda chitsogozo chake chasonyeza motsimikizirika kuti iwo sangathe kuchita zimenezo. Mkonzi wina anati: “Anthu ayesetsa kukhazikitsa mitundu yosiyanasiyana ya boma, komatu zoyesayesa zonsezo sizinaphule kanthu.”

14 Pa Yeremiya 10:23, timaŵerenga mawu a mneneri wouziridwayo kuti: “Inu Yehova, ndidziŵa kuti njira ya munthu sili mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.” Ndiponso, Salmo 146:3 limati: “Musamakhulupirira zinduna, kapena mwana wa munthu, amene mulibe chipulumutso mwa iye.” Kunena zoona, chifukwa chakuti ndife anthu opanda ungwiro, monga momwe akusonyezera Aroma 5:12, Mawu a Mulungu amatichenjezanso kuti tisamadzikhulupirire ife eni. Yeremiya 17:9 amati: “Mtima ndiwo wonyenga koposa.” Choncho, Miyambo 28:26 imati: “Wokhulupirira mtima wakewake ali wopusa; koma woyenda mwanzeru adzapulumuka.”

15. Kodi nzeru yotitsogolera tingaipeze kuti?

15 Kodi nzeru imeneyi tingaipeze kuti? “Chiyambi cha nzeru ndicho kuopa Yehova; kudziŵa Woyerayo ndiko luntha.” (Miyambo 9:10) Ndi Yehova yekha amene ali ndi nzeru imene ikhoza kutitsogolera m’nthaŵi zoopsa zino. Ndipo akupereka nzeru yake kwa ife mwa Malemba Oyera, omwe anawauzira kuti atitsogolere.​—Miyambo 2:1-9; 3:1-6; 2 Timoteo 3:16, 17.

Mtsogolo mwa Ulamuliro wa Anthu

16. Kodi ndani amene amadziŵa zamtsogolo?

16 Nanga kodi Mawu a Mulungu amatiuzanji ponena za mtsogolo? Amatiuza kuti mtsogolo simudzafanana mpang’ono pomwe ndi zimene munthu wachita kumbuyoku. Choncho lingaliro la Patrick Henry linali lolakwa. Ndi Yehova Mulungu yekha amene adzakonza tsogolo la dziko lapansili ndi la anthu okhalamo, osati munthu wina aliyense ayi. Chifuniro chake chidzachitika padziko lapansi, osati chifuniro cha munthu aliyense kapena mtundu uliwonse wa m’dzikoli. “Muli zolingalira zambiri m’mtima mwa munthu; koma uphungu wa Yehova ndiwo udzaimika.”​—Miyambo 19:21.

17, 18. Kodi chifuniro cha Mulungu nchotani ponena za nthaŵi yathu?

17 Kodi chifuniro cha Mulungu nchotani ponena za nthaŵi yathuyi? Akufuna kuthetsa dongosolo lilipoli lachiwawa ndi makhalidwe oipa. Ulamuliro woipa wa anthu umene wakhalapo zaka mazanamazana udzaloŵedwa m’malo posachedwapa ndi ulamuliro wa Mulungu. Ulosi wa pa Danieli 2:44 umati: “Masiku a mafumu aja [amene alipo lero] Mulungu wa Kumwamba adzaika ufumu [kumwamba] woti sudzawonongeka ku nthaŵi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse, nudzakhala chikhalire.” Ufumuwo udzachotsanso zisonkhezero zoipa za Satana Mdyerekezi, chinthu chimene anthu sangathe kuchita. Satanayo sadzalamuliranso dzikoli mpaka kunthaŵi yosatha.​—Aroma 16:20; 2 Akorinto 4:4; 1 Yohane 5:19.

18 Onani kuti boma lakumwambalo lidzaphwanya ndi kuchotseratu ulamuliro uliwonse wa anthu. Ulamuliro wa dzikoli sudzapatsidwa kwa anthu. Kumwamba, awo amene amapanga Ufumu wa Mulungu adzayang’anira zinthu zonse za padziko lapansi kaamba ka ubwino wa anthu onse. (Chivumbulutso 5:10; 20:4-6) Padziko lapansi, anthu okhulupirika adzalabadira malamulo a Ufumu wa Mulungu. Uwu ndiwo ulamuliro umene Yesu anatiphunzitsa kuupempherera pamene anati: “Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano.”​—Mateyu 6:10.

19, 20. (a) Kodi Baibulo limafotokoza motani ponena za makonzedwe a Ufumu? (b) Kodi ulamuliro wake udzachitanji kwa mtundu wa anthu?

19 Mboni za Yehova zimakhulupirira Ufumu wa Mulungu. Ndiwo “miyamba yatsopano” imene mtumwi Petro analemba za iyo kuti: “Monga mwa lonjezano lake tiyembekezera miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano mmenemo mukhalitsa chilungamo.” (2 Petro 3:13) “Dziko latsopano” ndilo mtundu watsopano wa anthu amene adzalamuliridwa ndi miyamba yatsopano, Ufumu wa Mulungu. Ameneŵa ndiwo makonzedwe amene Mulungu anavumbula m’masomphenya kwa mtumwi Yohane, yemwe analemba kuti: “Ndinaona m’mwamba mwatsopano ndi dziko latsopano; pakuti m’mwamba moyamba ndi dziko loyamba zidachoka . . . Ndipo [Mulungu] adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa; zoyambazo zapita.”​—Chivumbulutso 21:1, 4.

20 Onani kuti dziko latsopano limenelo lidzakhala lolungama. Anthu onse osalungama adzachotsedwa mwa kuloŵererapo kwa Mulungu pankhondo ya Armagedo. (Chivumbulutso 16:14, 16) Ulosi wa pa Miyambo 2:21, 22 umati: “Oongoka mtima adzakhala m’dziko, angwiro nadzatsalamo. Koma oipa adzalikhidwa m’dziko.” Salmo 37:9 likulonjeza kuti: “Ochita zoipa adzadulidwa: koma iwo akuyembekeza Yehova, iwowa adzalandira dziko lapansi.” Kodi simungakonde kukhala m’dziko latsopano lotero?

Khulupirirani Malonjezo a Yehova

21. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kukhulupirira malonjezo a Yehova?

21 Kodi tingakhulupirire malonjezo a Yehova? Mvetserani zimene iye akunena kupyolera mwa mneneri wake Yesaya kuti: “Kumbukirani zinthu zoyamba zakale, kuti Ine ndine Mulungu, ndipo palibenso wina; Ine ndine Yehova, ndipo palibenso wina wofanana ndi Ine; ndilalikira za chimaliziro kuyambira pachiyambi, ndi kuyambira nthaŵi zakale ndinena zinthu zimene zisanachitidwe; ndi kunena, Uphungu wanga udzakhala, ndipo ndidzachita zofuna zanga zonse.” Mbali yomaliza ya vesi 11 imati: “Ndanena, ndidzachionetsa; ndinatsimikiza mtima, ndidzachichitanso.” (Yesaya 46:9-11) Inde, tingakhulupirire Yehova ndi malonjezo ake monga kuti malonjezo amenewo akwaniritsidwa kale. Baibulo limanena za zimenezo kuti: “Chikhulupiriro ndicho chikhazikitso cha zinthu zoyembekezeka, chiyesero cha zinthu zosapenyeka.”​—Ahebri 11:1.

22. Nchifukwa ninji tingakhale ndi chidaliro chakuti Yehova adzakwaniritsa malonjezo ake?

22 Anthu odzichepetsa amasonyeza chikhulupiriro chimenecho chifukwa chakuti amadziŵa kuti Mulungu adzakwaniritsa malonjezo ake. Mwachitsanzo, pa Salmo 37:29, timaŵerenga kuti: “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.” Kodi tingakhulupirire zimenezi? Inde, chifukwa chakuti Ahebri 6:18 amati: “Mulungu sakhoza kunama.” Kodi dziko lapansili mwini wake ndi Mulungu, kotero kuti angalipereke kwa anthu odzichepetsa? Chivumbulutso 4:11 chimati: “Mudalenga zonse, ndipo mwa chifuniro chanu zinakhala, nizinalengedwa.” Choncho, Salmo 24:1 limati: “Dziko lapansi nla Yehova ndi zodzala zake zomwe.” Yehova analenga dziko lapansi, ndiye mwini wake, ndipo amalipereka kwa awo amene amamkhulupirira. Pofuna kulimbitsa chidaliro chathu m’zinthu zimenezi, nkhani yotsatira idzasonyeza mmene Yehova anasungira malonjezo ake kwa anthu ake m’nthaŵi zakale ndiponso m’tsiku lathu ndipo idzafotokozanso chifukwa chimene tingakhalire ndi chidaliro chachikulu chakuti iye adzateronso mtsogolo muno.

Mfundo Zobwereza

◻ Kodi ziyembekezo za anthu zayang’anizana ndi zinthu zotani m’mbiri yonse?

◻ Kodi nchifukwa ninji sitiyenera kudalira munthu kuti angadzetse tsogolo labwino?

◻ Kodi chifuniro cha Mulungu nchotani ponena za mtsogolo?

◻ Kodi nchifukwa ninji tili ndi chidaliro chakuti Mulungu adzakwaniritsa malonjezo ake?

[Chithunzi patsamba 10]

Baibulo limanena molondola kuti: “Sikuli kwa munthu . . . kulongosola mapazi ake.”​—Yeremiya 10:23

[Mawu a Chithunzi]

Bomba: chithunzi cha U.S. National Archives; ana ovutika ndi njala: WHO/​OXFAM; anthu othaŵa kwawo: UN PHOTO 186763/​J. Isaac; Mussolini ndi Hitler: chithunzi cha U.S. National Archives

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena