Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g89 5/8 tsamba 5-9
  • Nchifukwa Ninji Pali Vuto la Mtengo wa Kakhalidwe?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Nchifukwa Ninji Pali Vuto la Mtengo wa Kakhalidwe?
  • Galamukani!—1989
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Dongosolo la Chuma la Mitundu Yonse Losalimba
  • Kuwononga Ndalama kwa Maboma Kosawona Patali
  • Kukula kwa Chiŵerengero cha Anthu
  • Zifooko Zachibadwa m’Dongosololo
  • Gawo 1a: Kukhupuka ndi Kugwa kwa Dongosolo Lamalonda
    Galamukani!—1992
  • Kodi Pali Chiyembekezo Chotani Kaamba ka Kubwezeretsa Chuma?
    Galamukani!—1989
  • Kukwera kwa Mitengo—Mtengo wa Munthu
    Galamukani!—1989
Galamukani!—1989
g89 5/8 tsamba 5-9

Nchifukwa Ninji Pali Vuto la Mtengo wa Kakhalidwe?

KUCHOKERA ku Belgrade kufika ku Buenos Aires, kuchokera ku Lagos kufika ku Lima, kuchokera ku Manila kufika ku Mzinda wa Mexico, ndi kuchokera ku Washington, D.C., kufika ku Wellington, maboma akulimbana ndi kukwera kwa mtengo wa zinthu.

Nthaŵi zina maboma iwo eniwo amakhala m’zowawa zoipa zandalama. Ripoti lina likunena kuti “United States yapanga ngongole zochulukira m’zaka zisanu zapitazi kuposa m’mbiri [yake] yonse ya kumbuyoko.” Boma la mu Africa posachedwapa linayenera kubweza kuwonjezera malipiro koyembekezeredwa kwa nthaŵi yaitali. Ilo linapeza, ku kunyazitsidwa kwake, kuti Thumba Losunga Ndalama linalibe ndalama zokwanira kukwaniritsa bilu ya malipiro atsopanoyo. Mofananamo, m’dziko lalikulu la ku Latin America, liŵiro la kukwera kwa mtengo wa zinthu linali lalikulu kotero kuti boma linawopa kuti pofika kumapeto kwa 1988 likakhala losakhoza kupereka malipiro a ogwira ntchito zaboma oposa miliyoni imodzi.

Makonzedwe a zaka zisanu, kuchepetsedwa mphamvu kwa ndalama, kusawonjezera malipiro a anthu, kulamulira mitengo, ndi zothetsera mavuto a zachuma zina zikulengezedwa. Koma mavutowo ali ocholoŵanacholoŵana ndipo zothetsera ziri zosatsimikizirika. Kuti tichitire fanizo mavutowo, pano Galamukani! yandandalitsa kokha zina za zoyambitsa zenizeni za vuto la mtengo wa kakhalidwe.

Dongosolo la Chuma la Mitundu Yonse Losalimba

Kudalirana kwa dziko lonse. Monga mmene katswiri wodziŵa za ndalama wa mitundu yonse analongosolera kuti: “Dziko liri limodzi. Chuma chathu ndi cha dziko lonse. . . . Lingaliro lakuti chothetsera chingakhale cha mbali imodzi m’chuma cha dziko lonse liri lopanda pake.” Mwachitsanzo, kugwa kwa malonda m’maiko a Kumadzulo kumatumizidwa mwamsanga ku maiko osaukirako, omwe amapeza kuti palibenso ofuna kugula zopangidwa zawo. Mofananamo, kukwera m’chiwongola dzanja mu United States kumatanthauza kuti mitundu ya ku Latin America ndi Africa idzakhala ndi mavuto owonjezereka ndi kulipira mitengo ya chiwongola dzanja pa ngongole zawo. Kulankhula mwachisawawa, kusauka kokulira kumene dziko liri, kumatanthauzanso chisonkhezero chochepera chimene lidzakhala nacho pa mkhalidwe wa zachuma wa m’dziko lonse, koma limakhalanso chandamale chokulira ku nyengo zosayenerera zachuma.

Kusinthasintha m’mitengo ya zinthu za pa msika kumawunikira mtundu wa kugwedezeka kwa chuma cha dziko, limodzinso ndi kudalirana kwake. Osungitsa ndalama anali amantha kwenikweni ponena za ziyembekezo zachuma, kotero kuti ziŵerengero zochepera koposa za malonda a U.S. kaamba ka August 1987 ndipo mothekera ndemanga yosasangalatsa yopangidwa ndi nduna yosunga chuma zinanenedwa kukhala zokwanira kuyambitsa kugwa kwa msika wa dziko lonse mu October 1987.

Vuto lowopsya la ngongole la United States, limodzi ndi kusakhoza kapena kusafunitsitsa kwa mphamvu za zachuma zazikulu kugwirizanitsa lamulo la zachuma, kumachipangitsa icho kukhala chosayembekezereka kuti chidaliro chidzabwezeretsedwa mwamsanga. Akumalozera ku mkhalidwewu, katswiri wa zachuma Stephen Marris anachenjeza kuti: “Tiri m’mavuto. Palibe njira yopepuka yochokera mu iwo.”

Kusinthasintha kwa mitengo. M’zaka za posachedwapa pakhala kusinthasintha kodabwitsa kwa mitengo mu mafuta, zitsulo, ndi zinthu zina zofunikira. Kukweza kwa mwadzidzidzi kwa mitengo ya mafuta mu ma 1970 kunapangitsa kukwera kwa mtengo wa zinthu kofalikira ndipo kunayambitsa kugwa kwa chuma cha dziko lonse. Maiko Otukuka Kumene amene satulutsa mafuta mwapadera anayambukiridwa moipa.

Mu ma 1980 pakhala kutsika kwakukulu m’mitengo ya zinthu zambiri. Ichi chatsekereza moipa chuma cha maiko osauka kwenikweni amene katundu wawo wotumizidwa kunja amapangidwa mokulira ndi zotulutsidwa zoterozo. Maiko onga ngati Mexico ndi Nigeria, omwe amadalira kotheratu pa kutumiza kunja mafuta, akumanizananso ndi kugwa kokulira m’miyezo ya kakhalidwe chifukwa cha kutsika mitengo kwa mafuta. Kusinthasintha kwa mitengo koteroko kungagwetse makonzedwe abwino koposa a zachuma.

Kuwononga Ndalama kwa Maboma Kosawona Patali

Kuwononga ndalama kwa zankhondo. Chiwonkhetso chonse cha ndalama zowonongedwa zadziko lonse m’zankhondo kaamba ka 1987 chikuyerekezedwa ku chifupifupi madola triliyoni imodzi. Ichi chiri chofanana ndi chifupifupi $1.8 miliyoni pa mphindi imodzi! Simaiko olemera okha amene akuthera ndalama pa zida zankhondo; ena a maiko osauka koposa a m’dziko akonzekera chiwonjezeko cha 10 peresenti chaka chirichonse m’kuwononga ndalama ku zodzitetezera.

Katswiri wa zachuma John K. Galbraith, akumalongosola za chiyambukiro cha mayanjano ndi chuma cha kuwononga ndalama pa zankhondo kwa Maiko Otukuka Kumene, ananena kuti: “Awo amene amalipira kaamba ka zida zankhondo zimenezi ali osaukitsa a osauka. Izo zimagulidwa kuchokera ku ndalama zosasungidwira zida zankhondo zokonzekeretsedwa kuwongolera mtengo wa kakhalidwe, kuchokera ku ndalama za mkate weniweniwo.”

Maprojekiti a “njovu yoyera.” Chikunenedwa kuti mfumu ya ku Siam inali kupereka njovu yoyera kwa omuyang’anira omwe sanawakonde. Popeza kuti nyamayo inali kulingaliridwa kukhala yopatulika, iyo sikanapangidwa kugwira ntchito. Chotero kuisunga kwake kukabweretsa kusakaza m’zandalama kwa wolandira mphatso wopanda mwaŵiyo. M’zaka zaposachedwapa mitundu ya Kumadzulo mosazindikira yachita mbali ya mfumu ya ku Siam. Maprogramu awo a thandizo alipirira maprojekiti a luso la zopangapanga aakulu omwe mitundu yolandira yakhala yosakhoza kuwasunga m’kuwakonza.

“Njovu zoyera” zamtengo zimenezi, zopanda ntchito zimawononga mkhalidwe wa zachuma wa maiko osauka koposa: mabwalo a ndege abwino koposa pa amene ndege zimanyamukapo kokha mwa kamodzikamodzi, uvuni yokongola koposa yomwe singapange mkate chifukwa cha kusoweka kwa ufa wa tirigu, fakitale ya cement yaikulu yomwe mokhazikika imawonongeka chifukwa cha kusoweka kwa kuisamalira.

Nthaŵi zina maboma a Maiko Otukuka Kumene adziloŵetsa iwo eni m’ngongole zazikulu chifukwa cha kuwononga ndalama kosasamala pa maprojekiti onkitsa onga ngati malo opangira mphamvu ya magetsi, malo opangira mphamvu za nyukliya, kapena ngakhale mizinda yaikulu yatsopano.

Kukula kwa Chiŵerengero cha Anthu

M’maiko ambiri a dziko, kufulumira kwa kukula kwa chiŵerengero cha anthu kumathandizira ku kutsika kwa miyezo ya kakhalidwe. Nyumba, ntchito, masukulu, ndipo ngakhale kupangidwa kwa chakudya zimalephera kuyenda pa liŵiro limodzi ndi zofunika zomawonjezerekawonjezereka. Mexico, mwachitsanzo, chifukwa cha kuwonjezereka kosalamulirika kwa chiŵerengero chake cha anthu, ifunikira kupanga ntchito miliyoni imodzi pa chaka kokha kuti ichepetse liŵiro la kukwera kwa kusalembedwa ntchito kwake. M’maiko ambiri a ku Africa kukula kofulumira kwa chiŵerengero cha anthu—kopangidwa kukhala koipitsitsa chifukwa cha kusamukira ku mizinda—kwatsogolera ku kuwirikiza katatu kwa kugula chakudya kuchokera kunja kwa dziko ndipo kwathandizira ku kutsika kwa miyezo ya kakhalidwe mkati mwa zaka khumi zapitazo. Atate ena osowa chochita, osakhoza kupeza ntchito ndi kupereka kaamba ka mabanja awo aakulu, angowasiya iwo kapena adzipha.

Zifooko Zachibadwa m’Dongosololo

Mphamvu za msika zosawonedweratu. Kuneneratu za mtsogolo kwa zachuma kuli sayansi yoipa yosatsimikizirika. Vuto liri lakuti ngakhale m’chuma chopambana kuli kovuta kwa akatswiri kudziŵa mwachindunji chomwe chikuchitika, pamene kuli kwakuti m’chuma cha Maiko Otukuka Kumene—kumene dongosolo lolembedweratu kulibe—iko kuli kosatheka nkomwe. Ndipo ngakhale ngati akatswiri a zachuma angamvane pa mtundu weniweni wa mavutowo, iwo mosakaikira angapereke mayankho osiyana, mogwirizana ndi malingaliro awo andale zadziko kapena mayanjano. Kuipitsa nkhaniyo mowonjezereka, andale zadziko, omwe amapanga zigamulo zomalizira, amakhoterera kulabadira kokha uphungu wa chuma womwe amaupeza kukhala wowakomera.

Ponena za United States, yemwe kale anali mlembi wa zamalonda wa U.S. Peter Peterson analongosola kuti: “Kufika pachimake penipeni, mavuto athu sali a zachuma. M’malomwake, timatsekerezedwa ndi kusoweka kwathu kwa kuvomerezana kwa ndale zadziko. Sitimamvana nkomwe ngakhale pa mtundu wa mavuto athu a zachuma.”

Dyera losawunikiridwa. Dziko lirilonse limakhoterera kulondola zikondwerero zake zokulira mosasamala kanthu za chiyambukiro pa ena. Thandizo la zachuma, mwachitsanzo, lingakhale mu mtundu wa ziwiya zankhondo zapamwamba koposa, zotumizidwa ku dziko limene silingathe kudyetsa ngakhale nzika zake zonse. Mwachiwonekere, zolinga zadziko lothandiziralo ziri zachuma kapena ndale zadziko m’malo mwa umunthu. Zotsekereza za malamulo ochinga oikidwa ndi maiko a maindastri olemera kuti atetezere opanga zinthu awo amatsekereza zoyesayesa za maiko osauka koposa kugulitsa ngakhale zinthu zofunika zenizeni.

Maiko osatukuka amasuliza malo osungira ndalama a mitundu yonse chifukwa chokhala odera nkhaŵa kokha ponena za kubwezeranso chiwongola dzanja kwa mwamsanga. Maprojekiti ena anayenera kulekedwa chifukwa cha kusoweka kwa chirikizo la zandalama, kokha chifukwa chakuti iwo sadzatulutsa zobwezera za mwamsanga kaamba ka wobwereketsayo. Kukwera kwa mitengo ya chiwongola dzanja komwe mitundu yokongola imeneyi iyenera kupereka tsopano kuli mokulira chifukwa cha kuwononga ndalama kosakaza kwa mitundu ina yokhala ndi chuma chokulirapo kuposa mmene iyo iriri. Prezidenti Alfonsín wa ku Argentina analoza kuti m’zaka zisanu Latin America inali itatumiza ku United States ndi Europe ndalama zolingana ndi ma Marshall Plan aŵiri.a Gawolo, ngakhale kuli tero, liri loloŵetsedwa m’ngongole kwenikweni kuposa ndi kale lonse.

Chinyengo ndi umbombo. Maprezidenti a maiko ena a ku Africa ndi Asia apatsidwa mlandu wa kuba mabiliyoni a madola. Akuluakulu a polisi ndi nduna zotchuluka za malonda mu Latin America nawonso analoŵetsedwamo mu umbala wa madola mamiliyoni ochulukira. Unyinji wa ndalama wokulira umenewu kaŵirikaŵiri umachotsedwa ku maprogramu olinganizidwa kuwongolera mavuto ochulukira a anthu wamba. Chinyengo cha mlingo wa kumaloko pa miyezo yonse chimachepetsa mokulira chuma cha mitundu yosaŵerengeka, kuika mtolo wa ndalama wowonjezereka pa osauka ambiri omwe ayenera kulipirira icho.

Umbombo wosakhulupirika wa zamalonda umathandizirakonso ku vuto la mtengo wa kakhalidwe. Njira zotsendereza zogulitsira za makampani a mitundu yambiri a fodya, mwachitsanzo, zapambana m’kukakamiza mamiliyoni a anthu okanthidwa ndi umphaŵi kuwononga ndalama zochepera zomwe angakhale nazo pa ndudu. M’maiko ena otukuka kumene, ndudu zowopsyeza umoyo, zokhala ndi ululu wambiri zimagawiridwa mofala, ndipo ogula ambiri ali osazindikira ponena za ngozi ya umoyo. Dziko la mtengo wake la zamalimidwe latembenuzidwa kukhala lolimako fodya chifukwa cha msampha wa ndalama zakunja zofunika koposa, zomwe nthaŵi zambiri sizimakhalapo. Pa nthaŵi imodzimodziyo matenda ogwirizana ndi kusuta akuwonjezeka pa mlingo wokulira ndi kukwera kwa mtengo wa kakhalidwe.

Kubwereramo kwachidule kumeneku kwa zifukwa za vuto la mtengo wa kakhalidwe kumakwaniritsa kusonyeza chitokoso chowopsya choyang’anizana ndi maboma omwe akukalamira kuwongolera tsoka la chuma la nzika zawo. Prezidenti Mitterrand wa ku France, akulankhula m’magazini ya zachuma, anadandaula ponena za “dziko lomwe mokhazikika limasintha nsalu yoyala pansi kunsi kwa mapazi anu, kuikoka iyo ndi kuwopsyeza kukugwetsani.” Amuna a boma ndi akatswiri azachuma a Maiko Otukuka Kumene amadziŵa kuchokera ku chokumana nacho chowawitsa chenicheni chimene iye akutanthauza.

Kodi chimenecho chikutanthauza kuti palibe chiyembekezo kaamba ka kubwezeretsa kwa chuma? Kodi chuma cha dziko chiri chosakhoza kupereka kakhalidwe kabwino kaamba ka mtundu wonse wa anthu? Nkhani yotsatira idzayankha mafunso amenewa.

[Mawu a M’munsi]

a Marshall Plan inali programu yochirikizidwa ndi U.S. yokonzedwa kuthandiza kubwezeretsedwa kwa za malonda kwa Europe yosakazidwa ndi nkhondo. Kuyambira 1948 mpaka 1952 thandizo lofika ku mtengo wa 12 biliyoni linagawiridwa.

[Bokosi patsamba 8]

Vuto la Ngongole

Ngongole ya Mtundu

M’maiko ambiri zowonongedwa za boma zimapambana mokulira ndalama zolandiridwa. Kubwereka kopambanitsa komwe lamulo limeneli limafunikira kumatsogolera mkupita kwa zaka kukusonkhanitsika kwa kupereŵera kwa bajeti kokulira, nthaŵi zina kotchedwa ngongole ya mtundu. Kubwezera kwa ngongole imeneyi, limodzi ndi chiwongola dzanja, kumakakamiza maboma kupitiriza kubwereka, komwe kumawonjezera ndalama za chiwongola dzanja ndi kuyambitsa kukwera kwa mitengo. M’kuwonjezerapo, monga mmene magazini ya Time inalongosolera, maboma amakhala osafunitsitsa kuchepetsa ndalama zowonongedwa chifukwa chakuti “opanga masankho, pokhala anthu, amafuna mapindu owonjezereka ndi misonkho yochepera, ndipo andale zadziko, pokhala andale zadziko, amavomereza ku [zikhumbo za opanga masankhowo].” Chotero, tsiku la kukonza zinthu limaikidwa pambali, ndipo pa nthaŵiyi mtengo wa kakhalidwe umakwera.

Ngongole ya Mitundu Yonse

Kaamba ka zifukwa zosiyanasiyana, maiko ena amagula zinthu zochulukira ndi mautumiki kunja kwa dziko kuposa zomwe amagulitsa kunja kwa dziko, kutulukapo kupereŵera kwa ndalama za malonda a dziko. Kupereŵerako kuyenera kulipiridwa m’ndalama zomwe ziri zolandirika ku maiko ena, kaŵirikaŵiri m’madola kapena ndalama zina zamphamvu. Ndalama zimenezi ziyenera kaya kuchotsedwa ku thumba la ndalama zosungidwa pambali kapena kubwerekedwa ku maiko ena. Ngati thumba la ndalama zosungidwa pambali latsika mowopysa ndipo ndalama zokongola sizikupezeka, ziletso za katundu wogulitsa kuchokera ku maiko ena zingayenere kuyambitsidwa kapena ndalama ingachepetsedwe mphamvu. Miyezo iŵiri yonseyi imapangitsa kukwera kokulira m’mitengo ya katundu wogulidwa kuchokera ku maiko ena, zambiri za zimene zingakhale zofunikira za indastri ndi za wogula mofananamo.

Maiko Otukuka Kumene mwapadera ali ndi vuto la phindu la ndalama za malonda a dziko chifukwa chakuti, m’chifupifupi nkhani iriyonse, mtengo wa katundu yemwe amatumiza ku maiko ena unatsika mozizwitsa. Mwachitsanzo, mu 1960 tani ya kofi inakhoza kugula matani 37 a fetereza, pamene kuli kwakuti mu 1982 iyo inakhoza kokha kugula matani 16. Ziŵerengero zofananazo zikanaperekedwa kaamba ka cocoa, masamba a tii, thonje, mkuwa, chitsulo, ndi zotulutsidwa zina zoyambirira zomwe ziri zinthu zokulira zotumiza ku maiko ena za maiko osatukuka kwenikweni. Mokulira monga chotulukapo cha mikhalidwe yoipa ya malonda imeneyi, pa imene iwo amakhala ndi ulamuliro wochepera, podzafika mu 1987 maiko otukuka kumene anali ndi ngongole yowopsya ya $1,000 biliyoni. Mwala wamphero umenewo womangiriridwa m’makosi awo umaletsa moipa kubwezeretsedwa kwa chuma ndipo ngakhale kuwopsyeza kukhazikika kwa maboma ena.

The New York Times posachedwapa inachitira ndemanga kuti: “Nkhani imodzi yokha yomwe imagwirizanitsa Latin America iri ngongole . . . Vuto limeneli limapatsidwa thayo ndi maboma chifukwa cha kutchuka kwawo komanyonyotsoka ndipo limawonedwa monga mfungulo yoyenerera ya ndale zadziko yoyambukira mtsogolo mwawo mwa posachedwa.”

[Mapu patsamba 7]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Liŵiro la Kukwera kwa Mtengo wa Zinthu kwa Dziko 1980-85

(Yozikidwa pa El Mundo en Cifras, yofalitsidwa ndi The Economist)

■ 0 kufika ku 15%

■ 15 kufika ku 30%

■ 30 kufika ku 100%

■ kuposa 100%

■ ziŵerengero zomwe palibe

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena