Kodi Pali Chiyembekezo Chotani Kaamba ka Kubwezeretsa Chuma?
Mkati mwa kulamulira kwa Louis XVI wa ku France, mfumukazi yake, Marie Antoinette, chanenedwa kuti nthaŵi ina anafunsa minisitala woyang’anira chigawo cha ndalama wa banja lachifumu kuti: “Kodi mudzachita chiyani ponena za kupereŵera kwa ndalama, Monsieur le Ministre?” Yankho lake: “Palibe, Mayi. Iko kuli kwakukulu mowopsya.”
NGAKHALE kuti nthaŵi zasintha, nthanthi yapadera imeneyi ikuwonekabe kukhala yotchuka. Amuna a boma ndi akatswiri a zachuma mofanana amachitira chisoni ngongole yaikulu koposa ya mitundu yonse, kusalingana kowopsya kwa chuma pakati pa maiko olemera ndi osauka, ndi umphaŵi wowonjezereka m’maiko ambiri chotero. Koma zochepera ngati pali chirichonse zikuchitidwa—mavutowo ali owopsya mopambanitsa. Kodi chimenechi chimapanga nzeru ya zachuma?
Liwu lakuti “economics” (zachuma) limachokera ku liwu la Chigriki lakuti oikonomos, lomwe limatanthauza mdindo kapena wosamalira nyumba. Zachuma zadziko ziri kwakukulu maphunziro a mmene “nyumba” ya dziko imasamaliridwa. Kodi ndimotani mmene iyo ikusamalidwira?
Kuti tichitire fanizo, tiyeni tiyerekeze dziko lapansi kukhala unansi, ndipo mtundu umodzi ndi umodzi monga anansi. Mmodzi wa anansi wolemera koposa ali wowononga mosadziletsa ndipo ali ndi ngongole chifupifupi kwa aliyense, koma popeza ndi wochita naye malonda wabwino koposa, omukongoletsa ake akuzengereza kumufunsa kaamba ka kubwezera. Ena a mabanja osauka kwambiri ali mu ngongole mwakuya m’chakuti iwo ayenera kukongola ndalama kokha kuti alipire ndalama za chiwongola dzanja zokwera pa ngongole zawo. Pa nthaŵiyo, atate wa banja losowa koposa m’deralo wangodzichitira iyemwini ndi mabwenzi ake ku chakudya cha phwando lowononga ndalama, ngakhale kuti owerengeka a ana ake akusowa chakudya.
Mabanja olemera amadya bwino kwambiri ndi kuthera m’kutaya chakudya chambiri m’zotayilamo zinyalala. Iwo amawononga zochulukira pa zoŵeta zawo kuposa ndi mmene mabanja osawukirako angakhoze kuwononga pa ana awo. Kuchokera ku nthaŵi ndi nthaŵi iwo amakhala ndi kukumana kwa unansi kukambitsirana ponena za mavuto onse a m’deralo, koma palibe chirichonse chikuwoneka kuchitidwa. Kukwinjika kukukula pakati pa mabanja olemera ndi osawuka. Mwachidziwikire, chinachake chiri cholakwika mokulira ndi m’njira imene unansiwu ukusamaliridwa.
Winawake Wofunikira Kusamalira Chuma cha Chiwunda Chonse
Chisamaliro chabwino sichingachotsedwe ku makhalidwe. Monga mmene tawonera, dyera ndi umbombo pa mlingo wa mtundu, chigwirizano, ndi aliyense payekha zimathandizira mokulira ku vuto la mtengo wa kakhalidwe, makamaka m’maiko osauka. Kupanda chilungamo kwa zachuma kuli kokha chiwunikiro chimodzi cha dongosolo la zinthu losalungama.
Movomerezeka, palibe mayankho opepuka. Mavutowo ali okulira koposa kugwiridwapo ntchito ndi dziko limodzi, ndipo palibe bungwe la mitundu yonse lomwe liripo lokhala ndi mphamvu yofunikira kuchita ndi iwo. M’kuwonjezerapo, atsogoleri a dziko akusulizidwa kaamba ka kusowa chifuno cha ndale zadziko cha kuyang’anizana nawo mwachindunji.
Mosasamala kanthu za icho, mbiri yakale imalongosola wolamulira wina yemwe anali wodera nkhaŵa mwapadera ponena za tsoka la oponderezedwa pansi m’zachuma. Iye anayambitsa malamulo achindunji kuwatetezera iwo ndi kupereka zinthu kaamba ka iwo.
Wolamulira ameneyu anali yemwe anamasula Aisraeli kuchokera ku Igupto zaka zina 3,500 zapitazo ndi yemwe anawadyetsa iwo mozizwitsa ndi mana mkati mwa ulendo wawo wa zaka 40 kupyola m’chipululu. Mfumu yosawoneka imeneyi inatsimikizira kuti aliyense anali ndi zokwanira.—Eksodo 16:18; yerekezani ndi 2 Akorinto 8:15.
Pambuyo pake, pamene Aisraeli anafika mu Dziko Lolonjezedwa, malamulo operekedwa ndi Mulungu anatetezera osoŵa. Ngongole zopanda kuikapo chiwongola dzanja zinaperekedwa kwa awo amene anagwera mu nthaŵi zovuta. Osauka ankafunkha minda, minda ya zipatso, ndi minda ya mpesa. Ndipo eni ake anayenera kusiya chinachake kaamba ka ofunkhawo. Ndiponso, Mulungu analamulira Aisraeli achuma koposa ‘kutambasula dzanja lawo mooloŵa manja kwa ausiwa m’dzikolo.’—Deuteronomo 15:7-11.
Mulungu anasamalira nyumba ya Israeli m’njira yakuti mtundu wonse ukapambana, malinga ngati iwo anamvera malangizo ake. Omuimira ake, onga ngati Mfumu Solomo, anafunikira kutsanzira chitsanzo cha Mulungu. Ponena za Solomo, wamasalmo akulemba kuti: “Iye adzachinjiriza osauka koposa, adzapulumutsa ana a awo okhala m’kusowa . . . Adzamasula munthu wosauka woitanira pa iye, ndi awo ofuna thandizo, iye adzakhala ndi chifundo pa osauka ndi ofooka, . . . miyoyo yawo idzakhala ya mtengo wapatali m’maso mwake.”—Salmo 72:4, 12-14, The Jerusalem Bible.
Mosasamala kanthu za icho, Mulungu pambuyo pake ananeneratu m’Mawu ake kuti pakabuka vuto lowawitsa la mtengo wa kakhalidwe. Likumalongosola zenizeni za vuto la chuma limene potsirizira pake likakantha mtundu wa anthu, Baibulo linaneneratu kuti: “Malipiro a tsiku limodzi kaamba ka mkate umodzi.” (Chibvumbulutso 6:6, Weymouth, Kufalitsidwa Kwachisanu) Lerolino, umenewu ulidi mkhalidwe kaamba ka anthu osauka ambiri a dziko. Malipiro a tsiku limodzi lathunthu sakhoza ngakhale kukwaniritsa mtengo wa chakudya chimodzi.
Kubwezeretsa Kwenikweni kwa Chuma Kuwonekera
Yankho lokha ku mkhalidwe wa zinthu wochititsa chisoni umenewu linawunikiridwa ndi wopeza mphoto ya Nobel Willy Brandt. Iye ananena kuti: “Payenera kukhala kulingalira komakula kwakuti maiko osauka ndi olemera . . . ali omangiriridwa pamodzi ndi zikondwerero zawo zofala m’kupulumuka, ndi kuti mayankho adzafikiridwa kokha mwa kutenga kayang’anidwe kapatali ndi kafikiridwe ka dziko lonse.”
Chimenecho ndicho Mulungu ali nacho moyenerera m’lingaliro, kayang’anidwe kapatali ndi kafikiridwe ka dziko lonse. Mosiyana ndi olamulira aumunthu, Mulungu ali ndi ponse paŵiri chifuno ndi njira ya kubweretsera kubwezeretsedwa kwa chuma cha dziko lonse.
Mu ulosi umodzimodziwo wonena za vuto la zachuma, iye analozera kwa wolamulira amene anamuika, wolamulira wokhoza kuchiritsa mkhalidwewo. Iye akulongosoledwa kukhala atakhala pa kavalo “woyera” ndiponso monga mmodzi yemwe ‘akapita kugonjetsa.’ Ameneyu sali winawake kuposa Yesu Kristu, yemwe posachedwapa ‘adzagonjetsa’ kotero kuti afutukule ulamuliro wa Ufumu wa Mulungu monga boma lokha la mtundu wa anthu. Ufumu umenewu, m’manja mwa Yesu Kristu, uli njira ya Mulungu yothetsera, pakati pa zinthu zina, vuto la mtengo wa kakhalidwe.—Chibvumbulutso 6:2; yerekezani ndi Danieli 2:44.
Pansi pa ulamuliro wa Ufumu umenewu, wolozeredwa mu ulosi wa Yesaya monga “miyamba yatsopano,” Mulungu akulonjeza kuti: “Iwo sadzavutika mwachabe kapena kubala ana kaamba ka tsoka.” “Atumiki anga adzadya . . . ; atumiki anga adzamwa . . . ; atumiki anga adzasangalala.”—Yesaya 65:13, 14, 17, 23, The New English Bible.
Mamiliyoni amene lerolino akuvutikira mwachabe angatonthozedwe mtima ndi mawu amenewa. M’dziko latsopano la Mulungu, ana awo sadzamanidwa zofunikira zazikulu chifukwa cha tsoka la vuto la zachuma. Kudera nkhaŵa ponena za mtengo wa kakhalidwe kudzaloŵedwa m’malo ndi kukondwa m’chisangalalo cha kukhala ndi moyo.
Ngati inu mudzimva kuti malonjezo oterowo ali kokha loto Longolingalira, bwanji osakambitsirana ndi Mboni za Yehova pa nthaŵi yotsatira imene adzakuchezerani. Iwo adzakhala achimwemwe kukusonyezani kuchokera m’Malemba chifukwa chimene tingadalire mu yankho la Mulungu ku vuto la mtengo wa kakhalidwe.
[Chithunzi patsamba 10]
M’dziko latsopano la Mulungu, palibe amene adzakhala ndi njala kapena kusauka