Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g90 6/8 tsamba 23-24
  • Mfuti—Sizaamuna Okha

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mfuti—Sizaamuna Okha
  • Galamukani!—1990
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Ziŵerengero Zawo Zikuwonjezeka
  • Mfuti—Njira ya Imfa
    Galamukani!—1990
  • Mfuti—Njira ya Moyo
    Galamukani!—1990
  • “Mfungulo ku Ngozi”
    Galamukani!—1989
  • Mafunso Ochokera kwa Owerenga
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
Onani Zambiri
Galamukani!—1990
g90 6/8 tsamba 23-24

Mfuti—Sizaamuna Okha

M’DZIKO losatsa malonda, chithunzi cha mwamuna wojintcha wokwapatira mfuti chagwiritsiridwa ntchito kugulitsira zinthu zambiri. Icho chatchuka m’zonse—fodya, magalimoto, zovala, zida ndi zinthu zina zambiri, zolekezera kumaloto a wosatsa malonda okha.

Makamaka mu United States, amuna asonyezedwa kukhala osakhoza kukanganulidwa ku mfuti zawo. M’makwalala amizinda, zoumba zapangidwa za ngwazi zolakika zokhala ndi mfuti kaya mkwapa mwawo kapena kumbali kwawo. Ngakhale popanda mawu olembedwa, zithunzi zosonyeza nyengo yoluluzika ya Kumadzulo zimazindikiridwa mofulumira kuti nzokhala ndi mwamuna womangirira kamfuti m’chuuno mwake kophulitsa zipolopolo zisanu ndi chimodzi pa nthaŵi imodzi. Mitu ya mafilimu ambiri yaphatikiza liwu lakuti “mfuti.” Ziwonetsero za pa wailesi yakanema ndi m’zowonetsera makanema okomeza m’nyumba ali yakaliyakali ndi kutulutsa kusokosera kophulitsa mfuti kaŵirikaŵiri—amuna abwino ndi amuna oipa akumazikutumula m’zochitika zirizonse ndi m’mbali zonse. Anthu wamba amadzitama ndi mfuti yakumanja kapena mfuti m’dzanja lawo, ndi akufa enieni aligone pamapazi awo.

Koma akazi ambiri akuphatikizidwa m’mfuti. M’zaka zambiri zapita, mawailesi akanema akhala yakaliyakali ndi atifitifi achikazi ndi azondi akumawomberana mfuti ndi adani ncholinga chopheratu ndi chipambano chamfuti.

Iwo amakonda kulasa kwa kamfuti ndi mfuti, akumabulitsa chipolopolo chimodzi ndi chimodzi mwakuzitetekera pa zikwangwani zoimikidwa monga amuna ndi kumaziboola ndi zipolopolo pakati pa maso awo.

Motero siziyenera kukudabwitsani kudziŵa kuti mfuti zakumanja mwapadera zolinganizidwira akazi ziri kale m’masitolo ndipo zikugulidwa kwambiri. “Akazinu, simungadzole zonunkhiritsa za mwamuna,” analemba tero mtolankhani wina wamkazi, “chotero nkugwiritsiranji ntchito kalifafala ya mwamuna? Inu mufunikira kalifafala yopepuka, yopanda zoikaika zokoŵa zikadabo zanu, kalifafala yokongola koma yamphamvube. Mwinamwake mufunikira LadySmith ya mluli wa m’bowo wa mlingo wa .38 . . . yobiriŵira kwenikweni, kapena yotuwira, ya mluli wa utali wodzisankhira.” Katswiri wina anafotokoza lingaliro lake pa zimene akazi amafuna ku mfuti: “Mkazi amafuna mfuti kuwoneka yokongola. Iye amaifuna kukhala chinthu chowoneka bwino chimene angaike m’chikwama chake. Iye samafuna kuti isayenerane ndi botolo lake lamafuta ndi kalilore . . . Akazi ambiri amafuna zinthu kukhala zamtundu wofanana ndi zoyenerana. Iwo samafuna kuti iwoneke yoipa kapena yowopsya . . . Iye amaigulira chitetezo koma, panthaŵi imodzimodziyo, samafuna kuti iwoneke yonyansa.”

Mfuti zakumanja zina mwapadera zolinganizidwira chiphadzuŵa nzamluli wa m’bowo wa mlingo wa .38 zotenga zipolopolo zisanu ndipo zimakhala zamluli wa utali wa mitundu iŵiri—wamasentimita asanu ndi wamasentimita asanu ndi atatu—kuti ikwanire bwinobwino m’chikwama. Zina zimapangidwa ndi nthendere (zogwirira) zowongoka, zosalala bwino, ndipo zina zingakhale zamtundu wotumbuluka. “Nzokongola kwambiri,” anatero mkazi wina, “ndipo, ndiganiza nzosavuta kugwiritsira ntchito.” Ndiponso, pali mapangidwe atsopano azikwama zokhala ndi matumba mkati mwake opangidwira mfuti yakumanja ya akazi. “Mkazi wokhala ndi mfuti yakumanja wopanda chikwama chapadera akungodzifunira mavuto,” anatero mkazi wina. “Udzangopeza nyenyeswa za makeke ndi masiwiti mkati mwa mluli, kapena fodya, ngati umasuta, kapena chirichonse chimene chimakhalira kunsi kwa chikwama chamkazi.” Ena amawoneratu nthaŵi pamene kuwona mkazi wonyamula mfuti kudzakhala kofala ngati kuwona wonyamula sumbulele.

Ziŵerengero Zawo Zikuwonjezeka

Kuŵerengera kwaposachedwapa kwasonyeza kuti pakati pa 1983 ndi 1986, kukhala ndi mfuti kwa akazi mu United States “kunawonjezeka ndi 53 peresenti kukhala oposa 12 miliyoni.” Kuŵerengerako kunasonyezanso kuti m’zaka zitatu zimenezo, “akazi owonjezereka 2 miliyoni ankalingalira zogula zida.” M’magazine ena aakazi, chisamaliro chamachenjera chimaperekedwa ku kufunika kwakuti mkazi adzitetezere mwa kusonyeza chithunzi cha mkazi akubwerera kunyumba ndikupeza zenera loswedwa pakhomo loloŵera. Kodi iye amakhala yekha? Kodi ali ndi mfuti yodzitetezera atakumana ndi mpandu? Magwero achenjezo laulereli pamapeto pa kusatsako amakhala kampani yopanga mfuti, imene iri ndi mpambo watsopano wa mfuti zakumanja zokongola za akazi.

“Zosatsazi ziri ngati kuika mchere pa chironda,” anatero mkazi wina. Chifukwa nchakuti popeza kuti akazi ambiri amakhala okha kapena ali makolo osakwatiwa, amadzilingalira kukhala owopsyezedwa kwenikweni ndi upandu, kaŵirikaŵiri ndi chifukwa chabwino. M’mizinda yaikulu yambiri, kugwirira chigololo kukuwonjezeka. Akazi akutsompholedwa zikwama zawo—ambiri mwakuwopsyedwa ndi mpeni. Pali kuwukiridwa kwa akazi pa makwalala, m’malo oikamo magalimoto, ndi m’maofesi m’nthaŵi zamasana. Mafulati ndi nyumba zina, nyumba za akazi okhala okha, zimaloŵeredwa pamene okhalamo aligone. “Tiyenera kuphunzira kudzisamalira,” anatero mkazi wina, “chifukwa chakuti pamene tikukhala oyendayenda kwambiri m’chitaganya chomawonjezeka ndi chiwawa, tidzayenera kudzisamalira.”

“Ndinkabwerera kunyumba kuchokera kuntchito,” anatero mkazi wina yemwe anafunsidwa pa wailesi yakanema ya U.S. “Winawake anandigwira kuchokera kumbuyo. Anali ndi mpeni ndipo anandigwetsera pansi ndikutsomphola chikwama changa. Kuyambira pamenepo, ndinati ndiyenera kuchitapo kanthu.” Pambuyo pofunsira chilolezo choyenda ndi mfuti ndi kumayesera kulasa pa chandamale, kodi analingaliranji? “Mantha onse anatha. Ndinalingalira pandekha kuti, ndiri ndi mfuti, ndikhoza kulasa ichi ndipo iri yowopsya, sindimachita mantha. Ndi kachitsulo kameneka m’manja mwanga, ndingakhozedi kudzitetezera ndekha.”

Nkotsimikizirika kuti aka ndiko kalingaliridwe ka akazi oposa 12 miliyoni mu United States, ndipo ndani angadziŵe kuti ndi owonjezereka angati amene ali ndi zidazo popanda lamulo? Ziŵerengero za padziko lonse zingakhale zowopsya. Komabe, kodi kulingalira kumeneku, kuli chotulukapo cha kufufuza kochuluka kosonyeza zenizeni? Musanapite kukagula chida chodzitetezera inumwini, lingalirani zimene nduna za polisi ndi kupenda zikusonyeza.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena