Chivomerezo cha Oŵerenga Bukhu la Young People Ask
ENA anaganiza kuti anali pavuto. “Ndinaganiza kuti anafuna kutipatsa uphungu pa mayendedwe athu,” anatero msungwana wina wa zaka 15 zakubadwa wotchedwa Shereda. Ena analidi ndi mantha. Mnyamata wa ku Briteni wa zaka khumi zakubadwa wotchedwa Timothy akukumbukira motere: “Pamene ndinamva kuti ndinafunikira kuwasiya mayi ndi bambo wanga, sindinafune kupita.”
Nanga kodi chinawadetsa nkhaŵa nchiyani? Chinali chilengezo choperekedwa pa Lachisanu m’mawa pa Misonkhano Yachigawo ya “Kudzipereka Kwaumulungu” ya Mboni za Yehovaa chomwe chinati achichepere a zaka zapakati pa 10 ndi 19 anafunikira kukhala m’chigawo chokonzedwera iwo. Mantha onsewo anathetsedwa pamene bukhu lakuti Questions Young People Ask—Answers That Work linatulutsidwa ndi kugaŵiridwa kwaulere kwa achichepere onse opezekapo. Kodi kuyankha kunali kotani?
“Ndinalibe mawu; misozi inatsika pankhope panga.”—Mike.
“Ndinakhala kakasi pamene ndinawona chidziŵitso chabwino koposa m’bukhuli. Chenicheni chokha chakuti ilo linali mphatso yochokera ku Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova kwa achichepere chinali chitsanzo cha mmene iwo amatisamaliradi.”—Margie wa zaka khumi mphambu zisanu ndi zitatu.
Wa zaka khumi zakubadwa wotchedwa Naomi, amene atate ake anamwalira posachedwapa, anayamikira mwapadera kulandira bukhuli. Iye akukumbukira motere:
“Uwu ndiwo unali msonkhano waukulu woyamba umene banja lathu linapezekako popanda bambo wanga. Tsiku loyamba ndinali ndi chisoni kwenikweni. Koma chinandisangalatsa kudziŵa kuti abale athu ndi Atate wathu wakumwamba, Yehova, akutisamalira kufikira titalandiranso bambo wathu m’dziko latsopano.”
Mwachidule bukhuli nlodzala pafupifupi ndi theka la nkhani za “Achichepere Akufunsa Kuti . . .” zomwe zawonekera m’magazine a Galamukani! kuyambira mu 1982 mpaka 1989. Ilo liri ndi mitu 39, m’magulu a zigawo khumi. (Onani bokosi patsamba lotsatira.) Kodi pali phindu lanji lokhalira ndi chidziŵitso chonsechi m’bukhu lakumanja limodzi? Wachichepere wina akulongosola motere: “Kaŵirikaŵiri ndinadziŵa kuti ndinafunikira kufufuza nkhani zakumbuyo za ‘Achichepere Akufunsa Kuti . . . ’ kuti ndipeze thandizo ku vuto langa, komatu sindinali kuzipeza. Tsopano pali bukhu limene ndingalitenge nthaŵi iriyonse kuti ndiligwiritsire ntchito monga chitsogozo.”
Bukhu la Young People Ask lirinso ndi zithunzi zosangalatsa kwenikweni. “Ndimakondamo zithunzi za mitundumitundu,” watero Heather wa zaka 11 zakubadwa. Zithunzithunzizo zimasonyeza achichepere a padziko lonse lapansi. Wachichepere wa ku Canada anati: “Zithunzi zake zimamwereketsa kwenikweni ndipo zimaimira bwino malingaliro athu titayang’anizana ndi mavuto.” Pamenepo, nkosadabwitsa kuti achichepere ambiri anayamba kuŵerenga zamkati mwake atangolilandira.
‘Sindinaleke Kuliŵerenga’
Msungwana wa zaka 17 zakubadwa pa sitolo yogulitsa mabuku ya pa hotela, analemba motere:
“Tangotsala pang’ono kufika kunyumba kuchokera ku msonkhano wathu ndipo kwatsala ulendo wa galimoto wa maola anayi. Ndaŵerenga kale mitu khumi.”
Ena anakopedwa ndi ndandanda ya zamkati mwake motere:
“Pamene ndinaŵerenga ndandanda ya zamkati mwake, kunali ngati ndinkayang’ana pa mbiri ya moyo wanga weniweni. Mafunso ake ambiri anali amene ndinawafunsapo panthaŵi ina.”—Kathy wa zaka khumi mphambu zisanu ndi chimodzi.
Ngakhale anthu amene “samafuna kuŵerenga” anakopedwa:
“Sindimakonda kuŵerenga kwambiri, koma bukhuli nlabwino kwambiri kwakuti nditayamba kuliŵerenga, sindingaliike pansi. Ndaŵerenga pafupifupi bukhu lonselo m’masiku atatu.”—Jennifer wa zaka khumi mphambu zisanu.
“Sindine woŵerenga wabwino ndipo sindimaŵerenga kwambiri. Pamene ndinafika kunyumba kuchokera kumsonkhano, ndinali wotopa ndipo kunali kovuta kukhala maso. Koma ndinasanthula bukhuli, ndikuyamba kuliŵerenga, ndipo ndinaŵerenga mutu wathunthu! Kuchokera patsikuli, ndakhala ndikuŵerenga mutu umodzi tsiku lirilonse, kufikira usiku uno—pamene ndaŵerenga iŵiri!”—Tiffany wa zaka khumi mphambu zisanu ndi ziŵiri.
Ndipo panalinso osuliza:
“Ndinaganizira kuti ndinali wamkulu pang’ono kaamba ka mbali zina za bukhulo. Chotero ndinayamba kuŵerenga Chigawo 6, ‘Kugonana ndi Makhalidwe.’ Apa panandithandiza kwambiri kupanga zosankha zazikulu. Bukhuli liribe munthu wamkulu!”—Sabrina wa zaka khumi mphambu zisanu ndi zinayi.
Ndithudi, pamene ambiri alimaliza, alingalira kuti kuliŵerenga kamodzi nkosakwanira:
“Papita chaka chimodzi ndiri wobatizidwa, komatu zinthu zinaipirabe, ndipo ndinapsyinjika. Nthaŵi ina ndinathawadi panyumba! Chotero pamene ndinalandira bukhu latsopanoli, ndinaganiza kuti Yehova anadziŵadi chimene ndinkasowa. Nlabwino kwambiri! Ndaliŵerenga kale kaŵiri.”—J. S.
“Ndikulemba mawu a lemba lirilonse mkati mwa bukhuli kotero kuti kundipepukire kuliŵerenga bukhuli kachiŵirinso. Sindikukuza mawu ndi mkamwa: Bukhuli landipanga kukhala munthu wabwinopo.”—Aida wa zaka khumi mphambu zisanu ndi zitatu.
‘Sumaganizapo Kuti Ukulamulidwa Kuti Chita Chakuti’
Papita chaka chathunthu kuchokera pa kutulutsidwa kwa bukhu la Young People Ask, komabe ndemanga zachiyamikiro zidakalandiridwabe. Mosakaikira mbali ya chifukwa cha kupambanira kwake njakuti pamene kuli kwakuti nlolunjikitsidwa kwa achichepere, bukhuli silaubwana; ndipotu silinalembedwe m’njira yopangitsa aŵerengi ake kulingalira kuti likuwalalikira. Achichepere ena anafotokoza mwanjira iyi:
“Bukhuli nlosangalatsa. Pokhala lochilikizidwa ndi Mawu a Mulungu, Baibulo, ilo nlabwino kwambiri kuposa magazine a achichepere alionse.”
“Sumaganizapo kuti ukulamulidwa kuti chita chakuti; mmalo mwake, umagalamutsidwa ponena za kuthekera kulikonse ndi zotulukapo zake. Malingaliro a Yehova amasonyezedwa momvekera nthaŵi zonse ndipo amachilikizidwa ndi Malemba.”
Ambiri anafotokoza kuyamikira mtundu wa kalembedwe ndi chidziŵitso chimene linasonyeza malingaliro awo.
“Bambo wanga sanandisonyezepo mtundu uliwonse wa chikondi, koma uphungu wokhala m’bukhuli unamvekera ngati unachokera kwa bambo wachikondi amene amatilangiza kuti tipindule.”—Stefano, Italy.
“Maganizo amene ndinakhala nawo mofulumira anali akuti ndinkalankhula kwa winawake amene anandidziŵa kwenikweni osati kuti ndinkaŵerenga tsamba losindikizidwa.”—Myriam, Italy.
“Zitsanzo zambiri zimene zinagwiritsiridwa ntchito zinali ndendende ndi zochitika panyumba. Ndinathadi kuzigwirizanitsa zonsezo.”—Msungwana wachichepere.
“Ndidziŵa kuti m’Bungwe Lolamulira mulibe achichepere. Komabe, zonse zimene mumalemba ponena za achichepere nzolongosoka ndendende; kuli ngati ukulankhuzidwa ndi Yehova mwini mwachindunji.”—Aubree wa zaka khumi mphambu zisanu.
Silaachichepere Okha
Mitu yambiri imafotokoza mawu a mavuto oyang’anizidwa ndi Akristu achikulire, mavuto onga ngati manyazi, kuchita tondovi, kusukidwa, ndi ulova. Pamenepo, nkosadabwitsa kuti achikulire ambiri afotokozanso kuyamikira bukhuli. Mkazi wa minisitala woyendayenda wa Mboni za Yehova anati:
“Mwamuna wanga ndi ine tiribe ana obala tokha. Komabe, ndinapeza kuti nsongazo zinafotokozedwa m’njira yotipindulitsanso. Moyenerera bukhulo likadangokhala ndi mutu wakuti ‘Questions “People” Ask—Answers That Work!’”
Achikulire ena akuvomereza motere ndi mtima wonse:
“Muli masentensi, mawu, ndi malamulo amakhalidwe abwino omwe akhala opindulitsa kwambiri m’moyo wanga wachichepere wa zaka 41.”
“Simungaganizirepo kuti bukhu lolembedwera achichepere lingathandize mkazi wa zaka 61. Komatu linandithandiza kuganizira bwino ponena za kumbuyo ndi kuleka kusungirira zinthu kukhosi komwe ndakhala nako motsutsana ndi makolo anga.”
“Ndinazindikira kuti ‘achikulire amafunsa’ nawonso. Palibe chinthu chirichonse m’zaka zanga zambirizi monga Mkristu chimene chandithandizapo kwambiri kudzizindikira ndekha. Mwamalunji, ndiri wachichepere wa zaka 74.”
Pali makalata amene alandiridwanso kuchokera kwa makolo ambiri Achikristu:
“Ndiri ndi achichepere atatu, ndipo bukhuli linali yankho ku mapemphero anga. Zikomo kaamba ka kukhala kwanu thandizo kwa ife. Satana akuyesera chinthu chirichonse kukokera ana anga kunja. Komatu tsopano ndiri wokonzekeretsedwa zedi kuchita zomwe ndingathe mwaluso, zikomo kaamba ka bukhu lapanthaŵi yakeli.”
“Dongosolo lino limatikhwethemula tsiku ndi tsiku. Mwana wanga wamng’ono kwenikweni ngwazaka 12, ndipo chikondwerero chake m’zinthu zauzimu chakuladi m’zaka zapitazi. Nkovuta kukufotokozerani ubwino wa kumuona akugwirira ntchito kulinga ku ubatizo monga chotulukapo cha msonkhanowu ndi bukhu latsopanoli.”
“Misozi inatuluka m’maso mwanga pamene ana anga analandira makope awo. Palibe gulu lina lachipembedzo limene limasamalira achichepere ake chotere!”
“Ndine kholo lokha, ndipo nthaŵi zina ndimawopa ndipo ndimalingalira kuti ndine wosayenerera mokwanira kukhala kholo. Mwana wanga wamkulu ngwazaka 11 ndipo ali ndi mphunzitsi amene samamukonda. Nkotonthoza chotani nanga kupeza mutu m’bukhu la Young People Ask umene unachita ndi vuto limenelo!”
Ambiri anachitira umboni kukhutiritsa kwa mbali yakuti “Mafunso Okambitsirana” yopezeka pamapeto pa mutu uliwonse:
“Timaliŵerengera pamodzi bukhulo monga mbali ya phunziro lathu Labaibulo lokhazikika la banja. Ilo layandikitsa tonsefe pafupi. Ndinazindikira kuti ana amakhala aufulu ndi mafunsowo, ndipo liridi ndi kupindulitsa kwa kutsegula malingaliro kumene sikungafotokozedwe mopepuka.”
Mayankho Omwe Amagwiradi Ntchito!
Ndithudi, chodziŵitsa phindu la bukhuli sindicho kutchuka kwake koma kugwira kwake ntchito. M’kunena kwina, kodi mayankho ake amagwiradi ntchito? Achichepere ambiri amavomereza motenthedwa maganizo kuti amatero:
“Ndisanaliŵerenge bukhuli, ndinkapita ku Nyumba Yaufumu ndi amayi ndi mlongo wanga chifukwa chakuti sindikanatha kukhala ndekha panyumba. Ndinkakhala ndi moyo wapaŵiri. Tsopano zonsezi zasinthiratu kukhala wabwino.”
“Ungachisiye chowonadi, koma icho sichimakusiya. Pamsinkhu wa zaka 27, ndinayesa kubwerera ku Nyumba Yaufumu—ndekha, wamantha ndi wolapa. Ndinali ndi zizoloŵezi zoipa ndipo ndinalingalira kuti Mulungu sakandikhululukira. Koma mlongo wachikulire anandipatsa bukhu latsopano la Young People Ask. Ndinapeza kuti linafotokoza mavuto anga onse ndikusimba mochitira nawo. Ndinalira. Sindingafotokoze mokwanira mmene ndinayamikira bukhuli. Mayankho ogwiradi ntchito—ndipo anthuni!!!”
“Bukhuli linandipangitsa kulingalira mosamalitsa. Poyamba sindinadzilingaliredi kukhala mmodzi wa Mboni za Yehova. Ndinali ndi bwenzi lalikazi. Ndinkayenda ndi anthu akudziko. Ndipotu ndinali kuba. Koma pambuyo poŵerenga bukhuli, ndinazindikira kuti ndinkachita cholakwika m’moyo wanga. Ndinapemphera kwa Yehova kuti andikhululukire ndipo ndinamuyamikira pondipatsa ine bukhu latsopano labwinoli.”
Awa angokhala chitsanzo chokha cha makalata zikwi zambiri olandiridwa. Ife talimbikitsidwa ndi kusonkhezeredwa kwambiri ndi kuvomereza kwa achicheperenu. Mwachiwonekere, inu mumafuna kuchita zabwino, ndipo mumayamikira chitsogozo chimene Yehova amapereka mwachikondi m’Mawu ake. Nkwachiwonekerenso kuti mayankho ochokera m’Mawu a Mulungu amagwiradi ntchito!
Chotero mudzasangalala kudziŵa kuti mpambo wa “Achichepere Akufunsa Kuti . . . ” wa mu Galamukani! udzapitirizabe kupereka uphungu wolama, wozikidwa m’Baibulo pankhani zokudetsani nkhaŵa. Musaphonye nkhani ndiimodzi yomwe! Ndipo ngati simunaliŵerenge kale, liŵerengeni—ndipo liŵerengeninso—bukhu la Questions Young People Ask—Answers That Work.b Kambiranani za ilo ndi amkalasi mwanu. Ŵerengani malemba oikidwamo. Kambiranani mituyo ndi makolo anu. Gwiritsirani ntchito uphungu wake. Ndipo mosakaikira inu mudzavomerezana ndi Kent wa zaka 16 zakubadwa, amene anati: “Kuli ngati kukhala ndi kabukhu kakumanja kondithandiza kupyola zaka zovuta kwenikweni m’moyo wanga.”
[Mawu a M’munsi]
a Yochitidwa padziko lonse kuyambira mu June 1989.
b Ili mungalilandire mutalembera afalitsi a magazine ino.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 11]
Zamkatimu
Chigawo 1
Panyumba:
Kuchita ndi Ziŵalo Zabanja
Mutu Tsamba
1 Kodi Nchifukwa Ninji Ndiyenera
‘Kulemekeza Atate Ŵanga ndi Amayi Ŵanga’? 11
2 Kodi Nchifukwa Ninji Makolo Anga Samandimvetsetsa? 18
3 Kodi Ndingachititse Motani Makolo Anga Kundipatsa
Ufulu Wowonjezereka? 26
4 Kodi Nchifukwa Ninji Amayi ndi Atate Analekana? 34
5 Kodi Ndingachite Motani ndi Kukwatiranso kwa Kholo Langa? 42
6 Kodi Nchifukwa Ninji Mbale ndi Mlongo Wanga Ali Ovuta
Kwambiri Kugwirizana Nawo? 50
7 Kodi Ndiyenera Kuchoka Panyumba? 56
Chigawo 2
Inu ndi Ausinkhu Wanu
8 Kodi Ndingapange Motani Mabwenzi Enieni? 65
9 Kodi Ndingalake Motani Chitsenderezo cha Ausinkhu Wanga? 73
Chigawo 3
Kuyang’ana pa Mmene Mumawonekera
10 Kodi Mawonekedwe Ngofunika Motani? 82
11 Kodi Zovala Zanga Zimavumbula Zimenedi Ine Ndiri? 90
Chigawo 4
Kodi Nchifukwa Ninji Ndimalingalira Motere?
12 Kodi Nchifukwa Ninji Sindimadzikonda? 98
13 Kodi Nchifukwa Ninji Ndimachita Tondovi Kwambiri? 104
14 Kodi Ndingachititse Motani Kusukidwa Kwanga Kuchoka? 115
15 Kodi Nchifukwa Ninji Ndiri Wamanyazi Kwambiri? 121
16 Kodi Nkwachibadwa Kumva Chisoni Monga Momwe Ndimachitira? 127
Chigawo 5
Sukulu ndi Ntchito
17 Kodi Ndiyenera Kusiya Sukulu? 134
18 Kodi Ndingawongolere Motani Magiredi Anga? 140
19 Kodi Nchifukwa Ninji Achichepere Samaleka Kundivutitsa? 150
20 Kodi Ndingagwirizane Motani ndi Mphunzitsi Wanga? 158
21 Kodi Ndimotani Mmene Ndingapezere (ndi Kusunga!) Ntchito? 166
22 Kodi Ndiyenera Kusankha Ntchito Yophunziridwa Yotani? 174
Chigawo 6
Kugonana ndi Makhalidwe
23 Bwanji Ponena za Kugonana Ukwati Usanachitike? 181
24 Kodi Ndinganene Motani Kuti Ayi ku Kugonana Ukwati Usanachitike? 192
25 Psotopsoto—Kodi Ngwowopsa Motani? 198
26 Psotopsoto—Kodi Ndingalimbane Motani ndi Chisonkhezerocho? 205
27 Kuwona Mtima—Kodi Ndikodi Njira
Yochitira Zinthu Yabwino Kopambana? 212
Chigawo 7
Kupalana Ubwenzi, Chikondi, ndi a Ziŵalo Zosiyana
28 Kodi Ndingathetse Bwanji Kukhumbira? 219
29 Kodi Ndiri Wokonzekera Kupalana Ubwenzi? 225
30 Kodi Ndiri Wokonzekera Ukwati? 236
31 Kodi Ndingadziŵe Motani Ngati Chiri Chikondi Chenicheni? 242
32 Kodi Ndingachite Motani Kupanga Chitomero Chachipambano? 252
Chigawo 8
Msampha wa Mankhwala Oledzeretsa ndi Zakumwa Zoledzeretsa
33 Kumwa—Nkulekeranji? 262
34 Kodi Nkuneneranji Kuti Ayi ku Mankhwala Oledzeretsa? 272
Chigawo 9
Nthaŵi ya Kusanguluka
35 Kodi Zimene Ndimaŵerenga Ziri Nkanthu? 283
36 Kodi Ndingalamulire Motani Zizolowezi Zanga za Kuwonerera TV? 289
37 Kodi Nchifukwa Ninji Sindingathe Kusangalalako Nthaŵi Zina? 296
Chigawo 10
Mtsogolo Mwanu
38 Kodi Mtsogolo Mwandisungira Chiyani? 305
39 Kodi Ndingayandikire Bwanji kwa Mulungu? 311
[Bokosi patsamba 12]
‘Mbali Yapamtima Panga Yabukhuli Ndi . . .’
Achichepere ambiri anathirira ndemanga pambali ya zigawo khumi (zondandalitsidwa pansipa) za bukhu la Young People Ask zimene zinawathandiza mwapadera:
Panyumba: “M’chemwali wanga ndi ine timaputana nthaŵi zonse. Komatu bukhuli landithandiza kukhala wabwino kwa m’chemwali wanga. Ndipo titaputana, timapepesana ndipo timafotokozerana kuti sitinaganizire kunena zomwe tanenazo.”
“Ndinkaganizira kuti m’chemwali wanga ankapatsidwa chinthu chirichonse chimene iye anachifuna, komatu tsopano ndimazindikira kuti ndinali kumchitira nsanje. Ndazindikiranso kuti makolo anga ngosakondera koma akungoyesera pomwe angathe kutigawira chikondi chawo.”
“Ilo linandithandiza kudziŵa kuti amayi wanga ndi atate sanalekane chifukwa cha ine.”
Inu ndi Ausinkhu Wanu: “Linandithandiza kumvetsetsa kuti ngati ndikufuna bwenzi, nanenso ndiyenera kukhala waubwenzi. Ndiponso, ndaphunziranso kusakhala ndi ubwenzi ndi achichepere amene ali oyanjana nawo oipa.”
Kuyang’ana pa Mmene Mumawonekera: “Ndinali kuganiza kuti ndinali ndi thupi lolemera mopambanitsa, ndipo sindinathe kudya chirichonse kwa masiku angapo. Koma ndinkadyanso tsiku lotsatira ndikupezanso kulemera kuja. Ndinaganiza kuti ndinali woipa ndi wosakongola. Bwenzi langa lokondeka linandiuza kuŵerenga chigawo cha pa ‘mmene mumawonekera.’ Misozi inatuluka m’maso mwanga pamene ndinkaliŵerenga. Tsopano ndaika bwino zoyambirira zanga, ndipo ndikusumika pautumiki wanga kwa Mulungu—ndipo osati pa kawonekedwe kanga.”
Kodi Nchifukwa Ninji Ndimalingalira Motere?: “Ndinali wopsyinjika koipa, pamlingo wa kukhala ndi malingaliro akudzipha. Tsopano ndayamba kuyesera kuyang’anizana ndi mantha anga ndipo ndalandira thandizo laluso. Ndinatonthozedwa kwenikweni kuŵerenga kuti kudzakhala mapeto a ‘mantha okhazikikawa.’”
Sukulu ndi Ntchito: “Ndinali ndi mavuto ndi magiredi anga ndikunenezedwa nthaŵi zonse ku sukulu. Ndikukonzekera kugwiritsira ntchito uphunguwu kusukulu.”
Kugonana ndi Makhalidwe: “Pali kutsendereza kochuluka koikidwa pa achichepere kuti achite cholakwa, koma mwa kugwiritsira ntchito malamulo amakhalidwe abwino Abaibulo, ndingathe kutsutsa ausinkhu wanga.”
“Ndiri ndi vuto la kuchita psotopsoto, ndipo kukundichititsa tondovi kwenikweni. Koma ndidzapanga kuyesayesa kwamphamvu kugwiritsira ntchito uphunguwu ndikuyesera kukhala wachichepere wabwino koposa kwa Atate wanga wakumwamba.”
Kupalana Ubwenzi, Chikondi, ndi a Ziŵalo Zosiyana: “Ndakhumbira kwabasi msungwana wina kwanthaŵi ndithu tsopano. Sindimachita zopusa kapena kudzichititsa manyazi atakhalapo. Chikhalirechobe, ndinkalingalira mmene munafotokozera. Bukhuli linandithandiza kuzindikira kuti uku kunali kokha ubwana ndikuti sindinali wamkulu mokwanira kupalana ubwenzi.”
Msampha wa Mankhwala Oledzeretsa ndi Zakumwa Zoledzeretsa: “Ndiri watsopano kusukulu yapamwamba, ndipo anditambika kale mankhwala oledzeretsa. Bukhuli landithandiza kuwayankha kuti ayi.”
Nthaŵi ya Kusanguluka: “Ndinkapenyerera TV kuyambira Lolemba mpaka Lachisanu. Bukhuli linandithandiza kuchepetsa kupenyerera kwanga TV—kukhala pa Sande ndi Lachisanu pokha!”
Mtsogolo Mwanu: “Ndinkaganizira kuti Baibulo nlogwetsa ulesi—koma ndalekeretu! Ndimayesa kuliŵerenga mphindi 15 tsiku lirilonse!”
“Landithandizadi m’mapemphero anga. Tsopano ndingalankhule kwa Yehova monga bwenzi la pondapo nane mpondepo.”
[Zithunzi patsamba 10]
Gulu la achichepere a ku Falansa anatumiza chithunzi ichi (kulamanja) monga chizindikiro cha ‘kuteteza ndi kuchilikiza kwachikondi’ kwa Yehova ndi gulu lake pokonzekera bukhu la Young People Ask