Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g90 9/8 tsamba 7-9
  • Achichepere Amakono Akumana ndi Zitokoso za m’ma 1990

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Achichepere Amakono Akumana ndi Zitokoso za m’ma 1990
  • Galamukani!—1990
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Magwero Abwino Koposa a Thandizo kwa Achichepere
  • Baibulo ndi Makhalidwe Abwino a Achichepere
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Achichepere Amakono Chithunzi cha Padziko Lonse
    Galamukani!—1990
  • Gaŵirani Buku la Achichepere Akufunsa m’March
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1994
  • Mmene Mungapambanire Paunyamata Wanu
    Nsanja ya Olonda—2001
Onani Zambiri
Galamukani!—1990
g90 9/8 tsamba 7-9

Achichepere Amakono Akumana ndi Zitokoso za m’ma 1990

NOVEMBER 1985. Nthumwi zochokera m’maiko 103 zinakumana pamalikulu a Mitundu Yogwirizana kuti achotse “tsoka ladziko lonse lochititsa mavuto a achichepere m’dziko.”—UN Chronicle.

Zaka zisanu zapitapo, ndipo mavuto a achichepere adakakulirakulirabe kuposa ndi kale lonse. Kupikisanirana nthanthi za ndale zadziko, kutheredwa ndalama, ndi kusinthasintha zinthu zoti zikhale zoyambirira kuchitidwa kwadodometsa zoyesayesa zabwino za maboma za kugwirira ntchito pamodzi mokomera achichepere.

Mofananamo chipembedzo nachonso chalephera kukhala magwero ochilikiza zabwino. Kufufuza kwaposachedwapa kwa Gallup mu United States kwavumbula kuti chinkana kuti achichepere ambiri (pafupifupi 90 peresenti) amakhulupirira Mulungu (kapena mzimu wa kuthambo), ngochepa okha amene amalingalira chipembedzo kukhala chofunika kwenikweni m’miyoyo yawo. Ndiponso, chipembedzo chachita zochepa kapena kusachita nkanthu komwe kuthetsa mkhalidwe wa kugonana kopanda lamulo.

Kenaka pali otchedwa akatswiri—akatswiri a zamaganizo, akatswiri a zamayanjano, aphungu, ndi ena ofanana ndi awa—omwe amapereka uphungu kwa achichepere. Winawake ngwolama ndi wothandiza. Komabe, uphungu wawo umakhoterera kusumika pa zodetsa nkhaŵa zakuthupi izi: mavuto a zachuma odzetsedwa ndi mimba zotengedwa paubwana, kupeŵa AIDS, ngozi zakuthupi za kugwiritsira molakwa mankhwala ogodomalitsa. Iwo, ngati nkutchula nkhani zofunika kwenikweni zamakhalidwe zophatikizidwamo, amazifotokoza mwa apa ndi apo. “Akatswiriwa” kaŵirikaŵiri amakhala okhutiritsidwa ndi kutsatira zikhoterero za manenanena amakono ofala kapena kungobwerezabwereza mawu otchuka ofuulidwa, monga awa “Kugonana kwachisungiko” kapena “Mungoti ayi!”

Nanga bwanji ponena za makolo? Ambiri a awa nawonso ngwotanganitsidwa kwambiri ndi nkhani zakakhalidwe ka moyo. Pokhala osatsimikizira kuti ndi uphungu uti umene angaupereke kapena pokhala osamasuka kukambirana nawo nkhani zamanyazi, makolo ambiri amakhoterera kuzaza patabuka nkhani zamanyazi. Pamenepo, nkosadabwitsa kuti achichepere ambiri amatembenukira kwa anzawo opanda kuzoloŵera kaamba ka thandizo.

Magwero Abwino Koposa a Thandizo kwa Achichepere

Nangano, kodi ndimotani mmene achichepere angapezere mayankho opindulitsa a mafunso owazunguza? Mafunso onga awa: ‘Kodi ndiyesere kumwa mankhwala ndi zakumwa zoledzeretsa?’ ‘Bwanji ponena za kugonana ukwati usanachitike?’ ‘Kodi ndingadziŵe motani ngati chiri chikondi chenicheni?’ ‘Kodi mtsogolo mwandisungira chiyani?’

Ena angadabwitsidwe kumva kuti magwero abwino koposa a uphungu kwa achichepere ndiwo Mawu a Mulungu, Baibulo. Baibulo eti? Inde, ilo limanena zambiri kwa achichepere. (Onani Miyambo, mitu 1-7; Aefeso 6:1-3.) Kuwonjezera apa, ilo linauziridwa ndi Mlengi wathu, amene ali watcheru kwenikweni ndi “zokhumba zovuta za achichepere.” (2 Timoteo 2:20-22, Phillips; 3:16) Musananyalanyaze lingaliro lakuti bukhu lamakedzanali lingakhale lathandizo ku moyo m’ma 1990, lingalirani ichi: Kodi zingachitike kuti uphungu wambiri woperekedwa ndi “akatswiri” amakono udzaŵerengedwa ndi kulemekezedwa zaka 50 zokha kuchoka pano? Komabe, Baibulo lidakapitirizabe kutengedwa mosamalitsa kuchokera pa kulembedwa kwake zaka zikwi zambiri zapitazo!

Zowona, chitaganya cha anthu chasintha kwambiri kuchokera m’nthaŵi za Baibulo, koma chibadwa cha anthu sichinasinthe. Zokhumba za achichepere zidakali zofanana kwenikweni. Chotero Baibulo nlamakonobe monga kale. Ndipo limafika pamuzu wa mavuto ambiri omwe amadetsa nkhaŵa achichepere lerolino. Panthaŵi imodzimodziyo, ilo limapereka chiyembekezo chamtsogolo kwa achichepere.

Popeza kuti Baibulo limachokera kwa Mlengi wathu, ife tingayembekezere uphungu wake kukhala wogwira ntchito, wopindulitsa. Zokumana nazo zenizeni za moyo wa zikwi zambiri za achichepere Achikristu lerolino, omwe amatsatira chilangizo cha Baibulo, zimatsimikizira kuti ilo nloterodi! Kuti ithandize achichepere, Watch Tower Society yafalitsa bukhu lotchedwa Questions Young People Ask—Answers That Work. Ilo nlodzala ndi mfundo zambiri zodetsa nkhaŵa achichepere, ndipo uphungu wake ngwozikidwa pa Baibulo mokhazikika! Kuyamikira bukhuli kotenthedwa maganizo kwa achichepere kumachitira umboni osati ubwino wokha wa uphungu wa Baibulo komanso chenicheni chakuti achichepere amafunikira ndipo amapindula ndi chitsogozo cha Baibulo. Nkhani yotsatira iri ndi mawu ena apamtima operekedwa ndi achichepere padziko lonse.

Kaya ndinu wachichepere kapena wokalamba, inu muli ndi ntchito ya kuzoloŵerana ndi Baibulo. Mboni za Yehova zathandiza anthu mamiliyoni ambiri kuchita tero kupyolera m’makonzedwe aulere a phunziro Labaibulo lapanyumba, ndipo adzasangalala kwenikweni kukuthandizani. Mwa kukhala wozoloŵerana ndi kugwiritsira ntchito uphungu wa Baibulo, achichepere angaphunzire osati kokha mayankho opindulitsa ku mavuto amakono komanso njira yopezera chiyanjo cha Mulungu, amene akuitana achichepere kumtumikira.—Mlaliki 12:1.

[Bokosi patsamba 8]

Questions Young People Ask—Answers That Work

Panopa pali chitsanzo chokha cha uphungu wa Baibulo woperekedwa m’bukhuli pankhani zina zamakono.

Mliri wa AIDS: “Peŵani chisembwere. Chimo lina lirilonse limene mwamuna [kapena, mkazi] amalichita silimayambukira thupi lake: koma mwamuna wa liŵongo la chisembwere cha kugonana achimwira thupi lakelo.”—1 Akorinto 6:18, “Today’s English Version”; yerekezerani ndi Miyambo 5:3-20.

Kugwiritsira Molakwa Zakumwa Zoledzeretsa: ‘Usakhale mwa akumwaimwa vinyo, ndi ankhuli osusuka. Pakuti wakumwaimwa ndi wosusukayo adzasauka; ndipo kusinza kudzabveka munthu nsanza. Pa chitsiriziro chake [vinyo] aluma ngati njoka.’—Miyambo 23:20, 21, 32.

Ntchito: ‘Kodi upenya munthu wofulumiza ntchito zake? Adzaima pamaso pa mafumu, osaima pamaso pa anthu achabe.’—Miyambo 22:29.

‘Chirichonse mukachichita, gwirani ntchito mochokera mumtima, monga kwa [Yehova, “NW”], osati kwa anthu ai.’—Akolose 3:23.

Mantha a Kupululutsa kwa Nyukliya: ‘Atero Yehova amene analenga kumwamba, Iye ndiye Mulungu amene anaumba dziko lapansi, nalipanga; Iye analikhazikitsa, sanalilenga mwachabe; Iye analiumba akhalemo anthu.’—Yesaya 45:18; 55:10, 11; Mlaliki 1:4.

Kusatsimikizirika Kwachuma: ‘Iwo adzamanga nyumba ndi kukhalamo; ndipo iwo adzaoka minda yamphesa, ndi kudya zipatso zake. Iwo sadzamanga, ndi wina kukhalamo; iwo sadzaoka, ndi wina kudya; . . . Iwo sadzagwira ntchito mwachabe.’—Yesaya 65:21-23.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena