AIDS, ndi Lingaliro Lachinyengo la Chisungiko
MKAZI amene anapimidwa ndikupezedwa kukhala woyambukiridwa ndi kachirombo ka AIDS analemba motere, monga momwe anagwidwira mawu mu The New York Times ya June 16, 1990: “Ndine mkazi wachizungu wa zaka 36 wokwatiwa bwino, amene sindinayambukiridwepo ndi chindoko, chinzonono kapena matuza akumpheto, sindinagwiritsirepo ntchito crack, sindinakhalepo wogwiritsira ntchito anamgoneka kudzera m’mitsempha, sindinathiridwepo mwazi.”
Iye akuwonjezera kuti: “Chifukwa chakuti sindinagonanepo ndi aliyense wosakhala mwamuna wanga kuchokera pamene tinakwatirana, ichi chikutanthauza kuti ndakhala ndi kachiromboka kwa pafupifupi zaka zisanu popanda zizindikiro.” Kodi mkaziyu ali yekha? Kutalitali, monga momwe akunenera: “Ndikudziŵa pafupifupi akazi ambirimbiri a m’gulu langa okhala ndi ziyambi zambiri yamakhalidwe ofananawo.”
Nangano, kodi anthuwa ayambukiridwa bwanji ndi AIDS? Mkaziyu akufotokoza kuti: “Mwachiwonekere, ndinayambukiridwa ndi kachirombo kofooketsa mphamvu zotetezera thupi kupyolera m’chisembwere [ndisanakwatiwe]. . . . Mwamuna ameneyo mofananamo, akagwirizanitsidwa lerolino kukhala wogonana naye wowopsa, koma ichi sindinachidziŵe panthaŵiyo.”
AIDS kaŵirikaŵiri yafotokozedwa kukhala matenda olekezera kotheratu kwa amuna ogonana aziŵalo zofanana ndi ogwiritsira ntchito anamgoneka kudzera m’mitsempha. Koma malinga ndi zokumana nazo zake ndi chidziŵitso chodzimverera yekha, mkaziyu wakhutiritsidwa kuti lingaliroli “likupatsa anthu omveka m’chitaganya lingaliro lonyenga la chisungiko.”
Iye akumaliza kuti: “AIDS idzafalikira kwambiri kwa anthu ngati tipitirizabe kuganizira kuti imapezeka kwa anthu a m’magulu okhala pangozi okha, ndikuganizira kuti adzaitenga ndiwina, osati ine. Tonsefe tiri pangozi. Ngatitu ine ndingayambukiridwe ndi [AIDS], ndiko kuti mkazi aliyense (kapena mwamuna) angayambukiridwenso.”
Chomwe mkaziyu akuchinena, kuchifotokoza m’mawu ena nchakuti, mkazi kapena mwamuna aliyense wodziloŵetsa m’kugonana ukwati usanakhale—yemwe achita chisembwere—angayambukiridwe. Chotero, nkwanzeru chotani nanga kulabadira lamulo ili la Baibulo: ‘Thawani dama. Tchimo lirilonse munthu akalichita liri kunja kwa thupi; koma wachiwerewere achimwira thupi lake la iye yekha.’—1 Akorinto 6:18.