Achichepere Akufunsa Kuti . . .
Kodi Nchifukwa Ninji Ndiyenera Kuika Nzeru Kumaphunziro Pasukulu?
‘Ndiiko komwe, zambiri zomwe timaphunzira kusukulu zili chabe nthano. Palibe chimodzi cha izo chimene chiri ndi phindu lothandiza.’
‘Homuweki simandikondweretsa. Ndimakonda kwambiri zinthu zina, monga maseŵera ndi kupita kokacheza ndi mabwenzi.’
‘Ndidziŵa kuti ndidzaloŵa utumiki wanthaŵi zonse, choncho nkwanji kuika nzeru kumaphunziro pasukulu?’
KAŴIRIKAŴIRI achichepere amapereka ndemanga zimenezi polankhula za sukulu ndi homuweki. Mwina nanunso muli ndi malingaliro ofananawo.
Kunena zowona, atapatsidwa chosankha pakati pa maphunziro ndi zosangulutsa, achichepere ambiri angasankhe zosangulutsa. Ena amalakalakadi kusaphunzira konse. Samawawona mwamphamvu maphunziro; samawona kusiyana kulikonse kumene kuteroko kumapanga m’moyo. Kumbali ina, mwina inu mumafuna kupambana pasukulu koma simumakonda kwenikweni ntchito yanu yasukulu. ‘Sindimakonda kuphunzira basi,’ mungalingalire tero.
Mosasamala kanthu ndi malingaliro anu, zofuna zanu, kapena maluso, mukhoza kupeza chipambano pasukulu. Koma muyenera kusonkhezeredwa kuti mutero. Ndipo kupenda mapindu omwe mungapeze ngati muika nzeru kumaphunziro mwina kungawonjereze kwambiri chisonkhezero chanu.
Njira Yokhwimitsa Ubongo
Zambiri zimene mumaphunzira kusukulu tsopano zingawoneke kukhala zosafunika m’moyo wanu. Ngati sicholinga chanu kukaloŵa ntchito monga wasayansi, nkothekera kuti simudzawagwiritsira ntchito kwambiri mtsogolo masamu a physics omwe munaphunzitsidwa ndi aphunzitsi anu. Ndiponso, mutakhala wachikulire, sikwenikweni kuti mudzafunikira kufotokoza mitundu ya aneni kapena kupeza ma angle a isosceles triangle tsiku ndi tsiku. ‘Chotero, kodi nkuphunziriranji zonsezo?’ inuyo mungafunse motero.
Kunena zowona, sukulu imakupatsani mwaŵi wakudziŵa bwino zinthu zambiri ponena za masabujekiti osiyanasiyana, monga mbiri, literature, sayansi, geography, ndi masamu. Chidziŵitso chachikulu chimenechi chidzakulitsa kumvetsetsa kwanu dziko lokuzingani ndi kuyala maziko omangapo chidziŵitso chapadera chochuluka. ‘Wozindikira sawona vuto m’kuphunzira,’ imatero Miyambo 14:6.
M’bukhu lake lakuti Savoir étudier (Kudziŵa Mophunzirira), Robert Bosquet anapitiriza kulongosola kuti kuthekera kwa maganizo kwakuphunzira “kuyenera kutulukiridwa pang’onopang’ono ndi kulinganizidwa m’dongosolo logwira ntchito.” Anawonjezera kuti: “Aliyense adziŵa kuti ngwazi ya maseŵera imapeza zotulukapo zabwino kwambiri pambuyo pa kuyeseza kwa nthaŵi yaitali pamene imatulukira njira zogwiritsirira ntchito maluso ake mokwanira. . . . Kudziŵa mophunzirira kumatanthauza zimenezi: kugwiritsira ntchito kuthekera kwanu konse, kupeza zotulukapo zabwino koposa, ndi kusataya nthaŵi ndi kuyesayesa pachabe.”
Chifukwa chake homuweki ingatchedwe njira yokhwimitsa ubongo. “Ubongo . . . ndilukanelukane wamkulu wocholoŵana,” limatero bukhu lakuti How to Study, “ndipo kucholoŵana kwake ndi kulumikizana zitawonjezereka mpamene umagwira bwino ntchito.” Ntchito za kusukulu zingakuthandizeni kuwongolera maluso anu akusumika maganizo, kulingalira, kuloŵeza zinthu pamtima, kupenda vuto, ndi kupanga zosankha zanzeru.
Kukula Kwauzimu ndi Kwamaganizo
Zaka zanu zapasukulu zilinso nthaŵi yakukula kwauzimu ndi kwamaganizo. Mukukulitsa zizoloŵezi ndi mikhalidwe zimene kwakukulukulu zidzadziŵikitsa mtundu wa munthu wachikulire amene mudzakhala. Kodi mudzakhala wachangu, wakhama, wodziletsa, ndi waluso—munthu yemwe wolemba ntchito adzafuna? Kudziphunzitsa inumwini tsopano kuti mukapeze ntchito yabwino ndi zizoloŵezi zakuphunzira kudzakhala ndi mapindu a moyo wonse. (Yerekezerani ndi Miyambo 22:6.) Pakati pa zinthu zina, kungayambukire kwambiri mkhalidwe wanu wachuma wa mtsogolo ndi ziyembekezo zakuloŵa ntchito. Makampani ochuluka amagwiritsira ntchito cholembedwa cha munthu cha zipambano zake m’maphunziro monga njira yodziŵira kuthekera kwake kwa mtsogolo kwa kugwira ntchito.
Zizoloŵezi zanu zakuphunzira zimayambukiranso kukula kwanu kwauzimu. Yesu anaphunzitsa kuti munthu ayenera kulambira Mulungu ndi ‘nzeru zake zonse.’ (Marko 12:30) Zimenezi zimatanthauza kuti atumiki a Mulungu, achichepere ndi achikulire omwe, akafunikira kugwiritsira ntchito zolimba nzeru zawo kulandira chidziŵitso chimene Yehova amawapatsa ndi kumvetsetsa mmene angachigwiritsirire ntchito m’miyoyo yawo.—Yohane 17:3; 1 Timoteo 4:7.
“Ndimaziwona mwa achichepere ena a msinkhu wanga,” anatero Sylvie, msungwana wa ku Falansa. “Zizoloŵezi zakuphunzira zomwe anali nazo pasukulu zinapitirizidwa m’phunziro laumwini la zinthu zauzimu. Amene sanakonde kuphunzira pasukulu sanalinso okondweretsedwa m’phunziro laumwini la Baibulo.” Miyambo 10:4 imati: ‘Wochita ndi dzanja laulesi amasauka; koma dzanja la akhama lilemeretsa.’ Zimenezi zinakhaladi choncho kwa Sylvie m’lingaliro lauzimu. Zizoloŵezi zake zabwino zakuphunzira zinakupanga kukhala kosavuta kwa iye kuzamitsa chidziŵitso chake cha Baibulo. Zimenezi zinamkonzekeretsa kaamba ka ntchito yake monga mlaliki wanthaŵi zonse.—Yerekezerani ndi Salmo 1:2, 3.
Dziŵani Mmene Mungaphunzirire
Koma bwanji ngati mulibe mzimu wakuphunzira? Zindikirani kuti kusiyana kwakukulu pakati pa mwana wasukulu wochita bwino ndi wosachita bwino kaŵirikaŵiri kumakhala khama—osati luntha. “Ndinalibe luso lachibadwa lokulira mofanana ndi ana ena asukulu,” anavomereza motero Sylvie. “Kuti ndichite bwino pasukulu, ndinalimbikira kuikako nzeru kwambiri kumaphunziro kuti ndipeze magiredi okhutiritsa.” Ngakhale kuti sukulu inali yovuta kwa Sylvie, iye anapanga kuyesayesa kwakhama; sanangodziŵa kokha njira yophunzirira komanso yopezera chisangalalo pakutero. “Popeza kuti kuphunzira kapena kufufuza nkhani kunakhala chizoloŵezi,” iye akutero, “sikunali ntchito yaikulu yogwetsa ulesi. Ndinaphunzira kuichita mwachibadwa.”
M’bukhu lake lakuti How to Study, Harry Maddox anati: “Luso lokha nlosakwanira. Ana asukulu ambiri aluntha amalephera . . . chifukwa samachita ntchito yokwanira, kapena chifukwa chakuti sanadziŵe mmene angaphunzirire mofikapo.” Ndipo anawonjezera kuti: “Njira zogwira mtima za kuphunzira nzabwino kuzidziŵa osati kokha chifukwa cha zotulukapo zamwamsanga za kuphunzirako, koma chifukwa chakuti zizoloŵezi zanu za ntchito zidzakhalabe nanu m’moyo wanu wonse.”
Kaŵirikaŵiri anthu amakonda kuchita zinthu zimene amachita bwino—ndipo amapeŵa zinthu zimene samachita bwino. Mwinamwake nanunso mumada ntchito yakusukulu chifukwa chakuti simunakulitse kwambiri maluso anu akuphunzira kotero kuti muchititse ntchito yanu kukhala yosangalatsa. Ngati nditero, bwanji osasumika maganizo anu pa mmene mungaphunzirire? Chidziŵitso chothandiza chaperekedwa m’mutu 18 wa bukhu lakuti Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza.a
Yang’anani ku Nthaŵi ya Pambuyo pa Sukulu
Ana asukulu ambiri amanyalanyaza maphunziro awo kokha chifukwa chakuti angakonde kuchita zinthu zina—monga kukhala ndi nthaŵi yabwino. Koma Miyambo 21:17 imachenjeza kuti: “Wokonda zoseketsa adzasauka.” Zosangulutsa ndi kupuma zili ndi malo ake. (Mlaliki 3:1, 4) Komabe, pamene muli pasukulu, kuphunzira kuyenera kukhala chimodzi mwa zinthu zanu zoyamba. Zotulukapo zomwe mungapeze zimadalira kwambiri pa kuyesayesa komwe mungafune kukupanga. ‘M’ntchito zonse muli phindu,’ imatero Miyambo 14:23.
Zimenezi sizikutanthauza kuti inu kwenikweni mudzakonda maphunziro alionse a m’kalasi kapena ntchito yakusukulu imene mungapatsidwe. Koma mukhoza kuwona maphunziro anu monga njira yotsimikizirika yofikira cholinga chanu—kupeza chidziŵitso ndi maluso omwe adzakuthandizani kukhala ndi moyo watanthauzo ndi wopindulitsa. Kunena zowona, zofunika zophunzirira ndi mikhalidwe ya chuma zili zosiyana kwambiri m’maiko onse. Ngakhale nditero, achichepere ambiri amasiya sukulu asanapeze ngakhale maluso akuphunzira oyambirira enieni; amapeza kuti ali osakonzekera kapena osayeneretsedwa kaamba ka ntchito zochuluka. Ndipo kodi nchifukwa ninji? Chifukwa chakuti sanaike nzeru kumaphunziro pasukulu.
Musagwere mumsampha umenewu! Yang’anani ku nthaŵi ya pambuyo pa sukulu ndi kupanga makonzedwe a mmene mudzadzichirikizira inumwini mutamaliza sukulu. Mwina tsiku lina mungadzakhale ndi thayo lakusamalira banja. (1 Timoteo 5:8; yerekezerani ndi Miyambo 24:27.) Mofanana ndi achichepere ambiri pakati pa Mboni za Yehova, mwina inunso mukulinganiza kudzayamba ntchito monga mlaliki wanthaŵi zonse. Mudzafunikirabe kudzichirikiza inumwini ndipo mwina ngakhale banja lanu. Choncho lingalirani zakutsogolo. Musanamalize maphunziro, yesani kudziŵa ntchito zaganyu zomwe zimapezeka kwanuko. Kuika nzeru kwambiri kumaphunziro pasukulu kungakuthandizeni kukulitsa maluso ofunika opezera ntchito.
Mosasamala kanthu ndi zimene makonzedwe anu a mtsogolo ali, kuika nzeru kumaphunziro pasukulu kuli kwanzeru. Ayi, sikuti mudzatofunikira kupambana kalasi lonse. Koma mukhoza kudziŵa mmene mungakondere kuphunzira. Koma china chabwinopo nchakuti mukhoza kukulitsa chidziŵitso, maluso, ndi zizoloŵezi zimene zidzakupindulani m’moyo wanu wonse.
[Mawu a M’munsi]
a Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
[Chithunzi patsamba 24]
Maluso akuphunzira amene mumakulitsa pamene muli pasukulu adzakupindulani m’moyo wanu wonse